Bugwe la Copyright Society of Malawi (COSOMA), kudzera mwa wapampando wa bungweli a Chimwemwe Mhango, ati Lucius Banda sanagugepo chiyambileni kuyimba kwake zaka zoposa 30 zapitazo, zomwe zukuwonetseratu mphamvu zomwe Mulungu anamupatsa pa kapekedwe komanso kayimbidwe kake ka nyimbo ku Malawi.
Mu ma uthenga a kulira kwawo pa mwambo wa maliro a katswiri wa zimbale 20-yu pa bwalo la Balaka m’bomali, a Mhango ati mkofunika kuti dziko likhale ndi ndondomeko zabwino pa maluso ndipo anapempha mtsogoleri wa dziko kuti ayike ndondomeko zabwino kukonza malo owonetsela luso chifukwa ndi zomwe Soldier ankafuna,
Iwo anawonjezera kuti zonse zokhudza nyimbo za Lucius zili m’malamulo ndipo tsopano zili m’manja mwa banja ndipo kuti oyimba ena pamene akuyimba popeleka ulemu kwa katswiriyu akuyenela kutsatabe malamulo.
Mlembi wa chipani cha United Transformation Movement (UTM) a Patricia Kaliati ati chiyambileni limodzi mu chipani chawo cha UTM m’chaka cha 2017, a Banda anali odzipeleka, okhulupilika komanso ndi amene anathandizira kubweretsa anthu ochuluka ku chipanichi.
A Kaliati ayamika mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera pokhala thandizo kwa Lucius Banda kuyambira pamene anayamba kudwala. Iwo ati dziko likulira kwambiri ndipo mwezi wa June wakhala mwezi owawa ku banja lawo la UTM komanso dziko lino.
“Tikupempheni a President a Chakwera, Lucius Banda wasiya mkazi ndi ana timati tikupempheni kuti ngati nkotheka kuwapezera ntchito kuti imfa ya bambo wawo isawawe” a Kaliati anapempha.
Poyankhula Oyimilira mtsogoleri wa dziko lino yemwenso ndi nduna ya za maboma ang’ono a Richard Chimwendo Banda, ati Lucius Banda anagwira ntchito modzipeleka ndipo anathandizira ndondomeko zambiri za m’boma monga za NEEF,
A Chimwendo Banda ati nyimbo za Lucius Banda zinasunga ulaliki, utumiki, uneneli, kuyamika, chikondi ndipo zinalimbikitsa chikhalidwe m’dziko lino la Malawi.
Mfumu yayikulu Nsamala ya M’boma la Balaka ati oyimba Banda anali msangalatsi wa boma la Balaka ndipo ati boma la a Chakwera liyesetse kupeza chakudya kwa anthu a mdela lake chifukwa kuli njala popeza dziko ndi boma lokoma ndi lomwe msilikali wa amphawi Lucius Banda amkafuna.
Soldier Lucius Banda anamwalira pa 30 June mdziko la South Africa atadwala nthenda ya Ipsyo kwa kanthawi.