Azipembedzo alimbikitsidwa kuchilimika pa ntchito yogonjetsa TB

Advertisement
TB

Pomwe dziko lino likufunitsitsa kuthetsa matenda a chifuwa chachikulu cha TB pofika chaka cha 2030, langizo lapita kwa atsogoleri a zipembedzo komaso owatsatira awo kuti akhazikitse njira zosiyanasiyana zomwe zingathandizire kugonjetsa nthendayi.

Izi zakambidwa pa mkumano wa atolankhani komaso magulu ena okambirana za matenda a TB komaso khate omwe wachitika Lachinayi ndi Lachinayi ndipo unakozedwa ndi bungwe la National TB and Leprosy Elimination Programme (NTLEP) mothandizidwa ndi bungwe la Global Fund. 

Poyankhula pa mkumanowu, m’modzi mwa akuluakulu ku Ulama Council, Sheikh Ibrahim Mjatu, ati magulu a zipembedzo ali ndi udindo waukulu pa nkhani yothana ndi matendawa a TB komaso khate.

TB
Matekenya: Ndikofunika kuti atsogoleri achipembedzo azilimbikitsanso anthu kupita kuchipatala.

A Mtaju ati mwa zina kutenga gawo pa ntchito yothana ndi chifuwa cha TB komaso khate kungathandize kupititse patsogolo umoyo wabwino pakati pa anthu m’mizikiti komaso m’matchalitchi zomweso ati zitha kuthandizira kupititsa patsogolo chitukuko cha dziko lino. 

Iwo ati, “kuchipembedzo kuli anthu ochuluka kwambiri, choncho ngati atsogoleri kumeneku angamabweretse njira zosiyanasiyana pofuna kuthana ndi matenda amenewa, TB komaso khate idzakhala mbiri yakale m’dziko muno. Ifeyo ku chisilamu pali zambiri zomwe tikuchita pofuna kuthana ndi matendawa.”

M’mawu ake m’busa Chikondi Matekenya wa mpingo wa Seventh Day Adventist, wati ngakhale ena amayika patsogolo pemphero pa odwala matenda osiyanasiyana kuphatikiza TB ndi khate, ndikofunika kuti atsogoleri achipembedzo azilimbikitsaso anthu awo kupita ku chipatala kukalandira thandizo la mankhwala. 

A Matekenya ati mwa zina mpingo wa SDA unakhazikitsa njira zosiyanasiyana zomemera mamembala ake kudziwa zambiri za matenda a chifuwa cha TB komaso matenda a khate zomwe akuti zikupelekera mangolomera pa ntchito yothana ndi matendawa.  

M’modzi mwa akuluakulu a bungwe la NTLEP lomwe linayitanitsa mkumanowu Beatrice Nindi, watsindika za kufunika koti atsogoleri a zipembedzo akhale pa tsogolo pa ntchito yolimbana ndi matenda a TB komaso khate. 

Nindi wati, “ bungwe la NTLEP ndilodzipeleka kugwira ntchito ndi zipembedzo zonse pa ntchito yofuna kuthetsa matenda a TB komaso khate m’dziko muno.”

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.