Nduna yofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu ati thupi la wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima akaika ku mudzi kwawo ku Nsipe m’boma la Ntcheu Lolemba sabata ya mawa.
Poyankhura pa msonkhano wa atolankhani lero ku Lilongwe , a Kunkuyu ati mwambo onse udzayambira ku bwalo lamasewero la Civo Lachisanu ndipo Lamulungu, thupili lidzapita ku Kachisi wa Katolika ku St Patricks ku area 18 komwe kudzachitike mwambo wa mapemphero kenako kunyamura kupita nawo ku Ntcheu komwe akawaike m’manda.
Iwo ati komiti yomwe a pulezidenti Lazarus Chakwera akhazikitsa yoyendetsa malirowa komanso ena asanu ndi atatu yakhala ikugwira ntchito komanso kukumana ndi onse akubanja.
“Ku mmawa kuno tinakumana ndi akubanja kwa onse amene agweredwa zovutazi ndipo choti a Malawi akuyenera kudziwa ndichoti maliro onse ayendetsedwa ndi boma,” inatero ndunayi.
A Kunkuyu ati a kubanja komanso anamfedwa onse apemphedwa kuti apeze dotolo wapadera yemwe apime matupi onse kuti awone chomwe chinachititsa imfazi kupatura thupi la Abdul Lapukeni lomwe laikidwa kale m’manda ku mudzi kwawo ku Mangochi.
Kupatura apo, ati boma lawuza nduna ,osiyanasiyana kuti zikhale zikuimirira boma pa mwambo onse wokhudzana ndi maliro kufikira ataikidwa m’manda.
Ndunayi yapempha anthu onse m’dziko muno kuti apewe kugawana mauthenga omwe angabweretse chisokonezo komanso mpatuko pakati pa anthu zomwe zitha kukhala zolakwikwa.
A Chilima komanso anthu ena asanu ndi atatuwa anamwalira Lolemba pa ngozi ya ndege yomwe inachitika mu nkhalango ya Chikangawa m’boma la Mzimba.