Wa mlengalenga kachikena, Chakwera alunjika ku Bahamas ndi ku Switzerland

Advertisement
Lazarus Chakwera

Unduna owona za ubale wa dziko lino ndi mayiko ena walengeza kuti lero pa 10 June 2024, Chakwera anyamuka pa ulendo opita m’dziko la Bahamas komwe akukakhala nawo pa nsonkhano wa pachaka wa zamalonda omwe wakozedwa ndi AFREXIMBANK komanso Afri-Caribbean Trade and Investment Forum.

Malingana ndi undunawu, nsonkhanowu ukachitikira munzinda wa Nassau kuyambira Lachitatu pa 12 mpaka Lachisanu pa 14 June, 2024.

 Undunawu wati “Msonkhanowu ndi mwayi woti dziko la Malawi lipeze ndalama zambiri komanso kupeza mwayi wochita mgwirizano ndi ena pantchito yokwaniritsa masomphenya a Malawi 2063 omwe adakhazikitsidwa.”

Kupatula nsonkhanowu, m’dziko la Bahamas Chakwera akuyembekezeka kukakumana m’nkachipinda komata ndi atsogoleri osiyanasiyana andale komanso mabizinesi, omwe akakambirane nawo ndondomeko zofulumizitsira chitukuko cha dziko la Malawi.

Pakutha pa nsonkhano wa AFREXIMBANK ku Bahamas, Chakwera akapita ku Bürgenstock m’dziko la Switzerland komwe akuti ayitanidwa ndi mtsogoleri wa dzikolo a Viola Amherd.

Kumeneko nzika yoyamba ya dziko linoyi, ikakhala nawo pa zokambirana za atsogoleri a mayiko osiyanasiyana pa ndondomeko zomwe zingatsatidwe pofuna kuthetsa nkhondo ya pakati pa dziko la la Ukraine ndi Russia.

Undunawu wati Chakwera anyamuka pa bwalo la ndege la Kamuzu International lero Lolemba pa 10 June 2024, nthawi ya 5 koloko madzulo ndipo akuyembekezeka kubwelera m’dziko muno Lachiwiri sabata yamawa pa 18 June 2024.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.