Boma la Malawi lasaina pangano lofuna kuthana ndi kusintha kwanyengo

Advertisement
MOU on climate change investment

Boma la Malawi lasaina m’gwirizano omwe pa chingerezi ndi Memorandum of Understanding (MoU) ndi bungwe la African Climate Foundation (ACF), omwe ndi ofunika kwambiri pankhani zokhudzana ndi kusintha kwa nyengo.

A Colleen Zamba, omwe ndi mlembi wa pulezidenti ndi nduna za boma, wayamikira m’gwirizanowu ngati chivomerezo chofunikira komanso gawo lothandizira kuthana ndi vuto la kusintha kwa nyengo m’dziko muno.

Mwambo wosayinira m’gwilizanowu unachitikira ku ofesi ya pulezidenti ndi nduna za boma mu mzinda wa Lilongwe,

Zamba anati panganoli ndi chiyambi cha m’gwirizano pakati pa boma ndi ACF, kotero ndi chiyambi cha ntchito yothana ndi mavuto okhudzana ndi nyengo.  

Naye mlangizi wapadera ku bungwe la ACF, Irene Kerani anayamikira boma la Malawi kamba kolandilidwa bwino komanso zokambirana zosayinira panganoli.

Karani adatsimikiza zakudzipereka kwa ACF pankhani yogwira ntchito limodzi ndi boma ndi mabungwe aboma pofuna kulimbikitsa chuma cha dziko lino kudzera mu njira zothana ndi kusintha kwa nyengo. 

Panganoli lithandizira kupereka njira zoti dziko likhazikitse ma bizinesi ndicholinga chofuna kupititsa patsogolo chuma cha mphamvu ndi chokhazikika pothana ndi kusintha kwa nyengo. 

Panganoli lithandiziranso kupereka mwayi wopeza njira zatsopano zopangira ndalama pankhani yokhudza za nyengo zopindulira ma bizinesi a m’madera.

ACF ndi bungwe lothandiza anthu ku Africa lomwe limayang’ana kwambiri za nyengo ndipo limalandira thandizo kuchokera ku mabungwe osiyanasiyana opereka chithandizo padziko lonse lapansi. 

M’gwirizanowu ukusonyeza kuti dziko la Malawi liyenera kuchitapo kanthu pa nkhani yolimbana ndi kusintha kwa nyengo. 

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.