Ofesi ya Immigration ku Zomba yati ikugwira ntchito

Advertisement
Immigration Zomba

Mkulu wa nthambi yowona zolowa ndi zotuluka m’boma la Zomba, Superintendent Henry M’phuzula  wati ofesi yake ikugwirabe ntchito ndipo wati sakudziwa chilichonse chokhudza kunyanyala ntchito.

M’phuzula amayankhula izi ku ma ofesi anthambiyi pomwe atolankhani adapita kuti akadziwonere okha ngati akunyanyala ntchito kapena ayi.

Iye wati sadawuzidwe ndi akulu akulu ake kuti lero nthambiyi iyamba kunyanyala ntchito ndipo adati ntchito akugwira monga mwa masiku onse.

Koma a M’phazula adakana kuyankhulapo zambiri ndipo adawuza atolankhaniwa kuti ayankhule ndi m’neneri wanthambiyi kuti amve zambiri.

Pamene atolankhani amafika ku ofesi ya nthambi ya Immigration ya Zomba, adapeza ogwira ntchito pamolapa atangokhala kunja kwa ofesi akuwothera dzuwa.

Mphekesera zidamveka kuti ogwira ntchito kuma ofesi owona za anthu otuluka ndikulowa dziko muno ayamba kunyanyala ntchito Lolemba ati pofuna kukakamiza m’tsogoleri wa dziko lino Lazarusa Chakwera kuti achotse ntchito mkulu wa bungweli a Charles Kalumo ati chifukwa chokuti akumawazunza komanso sakugwira ntchito yake bwino.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.