Gaba wakalamba? Mtsutso wakula pa masamba amchezo

Advertisement
gabadinho mhango

Pabuka m’tsutso pa masamba amchezo potsatira zomwe wayankhula mphunzitsi wa timu ya mpira wa miyendo ya dziko lino a Patrick Mabedi omwe akuti Gabadinho Mhango wasiyidwa kutimuyi chifukwa osewelayu akukula.

 Lachiwiri Mabedi wauza nyumba zina zosindikiza nkhani m’dziko muno kuti Gaba, yemwe pano akusewera ku timu ya Moroka Swallows m’dziko la South Africa, sanamuitane kamba koti omwetsa zigoliyu akukura mu zaka zake.

 Mabedi wati kamba kakukulaku, Mhango akumalephera kugwirizana ndi osewera ena pa sisitimu yomwe timu yadziko linoyi ikumasewera.

 Nkhaniyi yabweretsa mtsutso waukulu pakati pa aMalawi makamaka pa masamba anchezo. Pomwe ena akugwirizana ndi Mabedi, ena asonyeza kusakhutira ndi zifukwa zomwe wapeleka mphunzitsiyu pakumusiya Gaba.

 “Mabedi usatinamize za Gaba kuti wakula, nkhani ndiyoti Gaba ali paubwezi ndi mwana wako nde sanje yakupweteka,” watelo Thomas Chiweza poyankhula za nkhaniyi pa tsamba lina pa fesibuku.

 Naye Brian Mandala wawonetsa kudabwa pa tsamba lina pa fesibuku ponena kuti ngati zili choncho ndikofunikaso kuti Mabedi asadzamuyitaneso osewera John Banda ku timu ya Flames kamba koti nayeso ndi wamkulu.

Kuwonjezera apo, Alick Archangel Kalirangwe Phiri wati, “Aaaaah mabedi usatilakwitse ife ndife anthu abwino koma umatiyamba dala, utisamale Gaba wakula ndekuti chani iwe nthawi yomwe unkasewera ku flames mesa unafika zaka 40 ukusewerabe. Ingonenani kuti you have issues with Gaba, age is just a number as long as his performance is fine akuyenera kusewera osati zako ukunenazo.”

 Mbali inayi anthu ena ati sakuona vuto ndikusiyidwa kwa osewerayu ponena kuti kupatula kukula komwe akunena Mabedi, Gaba samaonetsaso khalidwe labwino akayitanidwa ku timu ya Flames.

Nyede Kaimfa wati Mabedi ali ndi mphamvu zoitana osewera amene akumufuna ndipo wati “Osewera amene mukumuona wabwino kwainuyo, coach amamuona mosiyana. Siyani kumpasa pressure coach kuti asankhe player yemwe inuyo amakusangalatsani.”

 Pomwe mayiko akulimbirana malo m’chikho cha dziko lonse, Malawi isewera ndi Sao Tome and Principe masanawa pa bwalo la masewero la Bingu ku Lilongwe isananyamuke kupita ku Malabo komwe ikasewere ndi timu ya Equatorial Guinea Lolemba pa 10 June 2024. 

Advertisement