Mphunzitsi wamkulu wamangidwa atadya ndalama za mayeso a ophunzira a fomu 2

Advertisement
Malawi Students seating for Examination

Apolisi ku Area 24 mu mzinda wa Lilongwe ati amanga mphunzitsi wamkulu pa sukulu ya sekondale ya Eagles Academy, pomuganizira kuti anaba ndalama zomwe ophunzira adalipira pofuna kuti alembe nawo mayeso a fomu 2 omwe ayamba Lachiwiri.

Wachiwiri kwa m’neneri wa apolisi m’chigawo chapakati chakumadzulo, Sub Inspector Foster Benjamini, wati mphunzitsiyu yemwe dzina lake ndi Desmond Chidandale wazaka 30, akusungidwa mchitokosi kamba kakuba ndalama za ophunzira 6 zokwana K172,000.

Ophunzirawa adapereka ndalamazi kuti alembe nawo mayeso a chaka chino a fomu 2 omwe angoyamba lero.

Kumangidwa kwa m’phunzitsiyu kwadza kutsatira makolo anawa atakadandaula ku polisi za nkhaniyi ataona kuti ana awo alephera kulemba nawo mayeso lero.

Mphunzitsi wamkuluyu amachokera m’mudzi mwa a Chitedze kwa mfumu yaikulu Malili m’boma la Lilongwe.

Ndipo posachedwapa mphunzitsiyu akaonekera ku bwalo lamilandu komwe akayankhe pa mwandu wakuba.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.