Akubanja akusaka K43 miliyoni kuti thupi la malemu Hope Chisanu lifike ku Malawi

Advertisement
Hope Chisanu

Akubanja akhazikitsa ntchito yosonkhetsa ndalama zopitilira K43 miliyoni kuti thupi la malemu Hope Chisanu lifike ku mudzi kuno kuchokera m’dziko la America komwe wamwalilira sabata yatha.  

Malingana ndi zomwe taona pa intaneti patsamba la gofundme, Prophetess Dawa Kamanga wakhazikitsa ntchito yosonkhetsa ndalama zokwana $25,000 (K43.3 miliyoni) yomwe akuti ikufunika kuti thupi la malemuwa lifike ku Malawi kuno.

Patsambali mkazi wa malemu Chisanu, Vivian wapempha anthu akufuna kwa bwino kuti awathandize ndi kangachepe kuti thupi la katswiri pa zisudzoyu lidzayikidwe m’manda ku mudzi kuno.

“Ndikulemba izi kuti ndilimbikitse onse akufuna kwabwino kuti ayimilire ndi ine ndi ana anga, kuphatikiza banja lonse kuti thupi lake (Hope Chisanu) libwere kumudzi kuno.

“Pamodzi ndi banja lake lonse komanso abale ake kuno ku Malawi, komanso chifukwa cha mavuto azachuma omwe tili nawo okhudzana ndi mabilu akuchipatala komanso mtengo wonyamula thupi lake, tikusowa thandizo la ndalama kuti adzayikidwe m’manda kuno ku Malawi,” watelo Vivian.

Pakadali pano, ndalama zokwana $1,507 yomwe ndi pafupifupi K2.7 miliyoni, ndi yomwe yatoleledwa kudzera pa tsamba la gofundme.

Hope Chisanu yemwe wasiya mkazi ndi ana awiri, anamwalira Loweluka pa 1 June 2024 atadwala kwa nthawi yochepa m’dziko la United States of America komwe amakhala.

Chisanu wagwira ntchito ya uwulutsi ku wayilesi ya boma ya MBC ndipo kamba ka mawu ake opatsa chikoka komaso okhathamira, ankadziwika kwambiri ndi dzina loti “Uncle Bemberezi.”

Kupatula apo, malemuwa anali namatetule pa nkhani ya zisudzo ndipo anatenga nawo magawo akuluakulu m’ma kanema a ‘The Last Fishing Boat’ komaso yomwe yatulutsidwa posachedwapa ya ‘Is The President Dead?’.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.