Tikakonze malamulo Chakwera apitilize kuposela 2030 – Kathumba

Advertisement
Esther Cecilia Kathumba

Phungu wa nyumba ya malamulo wa dela la Lilongwe Mapuyu South Esther Cecilia Kathumba ati akapita kunyumba ya malamulo akawupanga mpando wa mtsogoleri wa dziko kuti ukakhale wa muyaya ndipo kuti a Lazarus Chakwera adzapitilize kutsogolera dziko la Malawi kupitilira 2030 komanso kuti a Chakwera adzausiye mpandowu mwa kufuna kwawo chifukwa cha ukalamba.

Phunguyu wayankhula izi lero pa mwambo otsekulira ntchito ya Millennium Challenge account 2 womwe ukuchitikira pa bwalo la Mzonde kwa mfumu yayikulu Kalolo m’boma la Lilongwe.

M’mawu ake phunguyu wati tsiku lina anapita ku state house ndipo anafunsa president Chakwera kuti mchifukwa chiyani akugawa zitukuko ku madela komwe kuli zitukuko kale ndiponso kwa omwe ankawasala pa zitukuko mbuyomu, koma mtsogoleri wa dzikoyu anawayankha kuti mulungu akanati adziwelengela mphulupulu bwezi ambiri pa dziko akulangika.

Mmawu awo Senior Chief kalolo ya m’boma la Lilongwe yapempha pamaso pa mtsogoleri wa dziko kuti ndondomeko ya chitukuko cha madzi ikafike ku Namitete komwe ndi ku malire kwa boma la Lilongwe ndi la Mchinji ndipo athu adzavotera a Chakwera chifukwa cha zitukuko zomwe akuchita.

Pa mwambowu Pali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko a Saulos Chilima, sipikala wa nyumba ya Malamulo, nduna ndi adindo ena a ku zipani komanso boma.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.