Mtumiki wati Jetu watenga njira yachitayiko, asiye kuyimba

Advertisement
Jetu

“Mama Jetu siyani njira ya kuchitayiko yomwe mwayiyamba, its too late for that. Dziko la pansi limapeleka sapoti pa zinthu zoyipa zakuchionongeko.”

Awa ndi mawu omwe mtumiki wina akuti watumidwa ndi Mulungu kupita kwa woyimba Jetu ndipo wati zonse zomwe zikuchitikira woyimbayu ndi matchera a satana osati m’dalitso.

Mtumikiyu yemwe akudziwika ndi dzina loti mvangeli Martha, watekesa masamba amchezo pomwe watulutsa kanema yomwe akuti ndi uthenga omwe watumidwa ndi Mulungu kupita kwa woyimba wa zaka 72 Christina Malaya yemwe watchuka ndi dzina loti Jetu.

Mukanemayi yomwenso ife tayiwona, mvangeli Martha wadzudzula Jetu kamba koyamba kuyimba atakula kale zomwe wati ndi njira ya chitayiko, ndipo wamuuza kuti asiye kuyimbako, alape komaso ayambe kumutumikira Mulungu.

M’tumikiyu wati unyinji omwe uli nyominyomi pambuyo pa woyimba Jetu ndi chifukwa choti; “dziko la pansi limapeleka sapoti pa zinthu zoyipa zakuchionongeko koma pa zabwino silipeleka sapoti ndipo limadana ndi anthu omwe akuchita zabwino. Mama nkwabwino kuti muyambe kuyenda ndi Yesu m’khilisitu kuti akhale mpulumutsi wanu.”

Apa mtumikiyu wati Jetu anakakhala kuti anayamba kuyimba nyimbo zauzimu sanakalandira sapoti yomwe akulandira pano zomwe wati ndichitsimikizo choti dziko la pansi limakondadi zinthu zauchimo.

Mvangeli Martha waneneratu kuti akudziwa kale kuti anthu ambiri amusambwadza kamba ka malangizo omwe wapelekawa koma iye wanenetsa kuti sakutekeseka kamba koti izi wamutuma ndi Mulungu.

Iye anatsiliza ndikunena kuti; “zomwe zikuchitikazi ndimatchera a satana mdyelekezi, simdalitso wa Mulungu. Mukakhala wina nthawi ino ndiye yofunika kuti mulape. kwamane akuchimva chonde muonetseni Jetu uthenga umenewu.”

Izi zikubwera patangodutsa ma sabata ochepa pomwe makosana a Podcast Malawi nawoso analangiza Jetu kuti asiye kuyimba ponena kuti gogoyu alibe lunso pamayimbidwe. Nkhaniyi inakwiyitsa anthu ochuluka.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.