Phungu wa Zomba Malosa afunira mafuno abwino ophunzira a Standard 8

Advertisement
PSLC Exams Zomba

Phungu wakunyumba yamalamulo wamdera la Zomba Malosa Grace Kwelepeta wafunira mafuno abwino ophunzira a standard 8 a sukulu zomwe zikupezeka m’dera lake omwe ayamba kulemba mayeso omaliza opitira ku sekondale omwe amayendetsedwa ndi Bungwe lomwe limawona zamayeso la Malawi National Examination Board (MANEB)

Kwelepeta walimbikitsa ophunirawa kuti alembe mtima ulipansi ndipo ayike Mulungu patsogolo panthawi yomwe akulemba mayesowo.

Grace Kwelepeta-MP
A Kwelepeta alimbikitsa ophunzila kuti ayike Mulungu patsogolo.

Iye wati ophunzira omwe adzakhoze bwino kupita ku sekondare adzalandira mphatso zosiyanasiyana zomwe pakadali pano sadazitchule ndipo wati adzaperekanso mphatso kwa m’phunzitsi yemwe adzakhozentse bwino mayeso ophunzira ake.

“Ndifunire mafuno abwino ophunzira onse omwe akulemba mayeso a standard 8 m’dera langa la Zomba Malosa ndipo ndafuna kulonjeza kuti ophunzira yemwe adzakhoze bwino kupita ku sekondale ndidzamupatsa mphatso,” anatero Kwelepeta.

Zaka zam’buyomu, phunguyu wakhalanso akupereka mphatso zosiyana siyana monga zikwama, zofunda ndi zina zambiri kwa ophunzira omwe amasankhidwa kupita ku sekondare zogonela komweko komanso wakhala akupereka mphatso kwa aphunzitsi omwe amakhonzetsa mayeso bwino.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.