Yadya 1 pa YouTube ndi Controller

Advertisement
Onesimus Malawi

Mtengo wautali salozerana ndipo nyimbo yomwe yadya nambala one pa YouTube ndi ija ya mkulu odikula uku akutudzula mbina maka ikafika paja akumati “She got me feeling like ah ah ah ah ah ah!” 

Tsopano nyimboyi yaoneredwa ka 1.4 miliyoni msabata ziwiri zokha zomwe ndizopatsa chidwi.

Sabata ziwiri zokha ndi zomwe zadutsa chitulutsileni kanema wa nyimboyi koma zikuonetsa kuti anthu ayilandira ndi manja awiri. 

Angakhale kuti kanemayu akupitilira kukondedwa chonchi, Onesimus anati nyimboyi kanema wake weni weni akuyembekezeka kutuluka ndipo uyu ndiwongoyeselera chabe.

Pakadali pano oyimba otchuka wa m’dziko la Nigeria wamgulu lomwe limkatchedwa kuti P-Square, wagwilitsapo kale nyimbo ya Controller pojambulira ka kanema wake pa TikTok.

Advertisement