Ikakuona litsiro siikata; khothi lakana Nankhumwa, atha kuchotsedwa pa udindo otsogolera zipani zotsutsa

Advertisement

Madzi akupitilira kuchita katondo kumbali ya a Kondwani Nankhumwa omwe pano khothi lawakaniraso pempho lawo lomwe amafuna khothilo lisamve pempho la chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) pa nkhani yofuna kuwachotsa pa udindo wa otsogolera zipani zotsutsa boma m’nyumba ya malamulo.

Nkhaniyi ikudza pomwe m’mbuyomu a Nankhumwa omwe ndi phungu wa dera la pakati m’boma la Mulanje, anatenga chiletso choletsa chipani cha Democratic Progressive kuwachotsa pa udindo wa otsogolera zipani zotsutsa boma m’nyumba ya malamulo.

Zitatele, chipani cha DPP nacho chinathamangira ku khothi kuti chikachotse chiletsochi, koma pomwe oweruza milandu Simeon Mdeza anali chile kufuna kumva pempho la chipanichi, a Nankhumwa anapempha khothi kuti lisamve pempho la chipani cha DPP.

Mwazina, a Nankhumwa kudzera kwa owayimilira awo a Wapona Kita komaso a Gift Katundu, anati anapempha khothi kuti lisamve pempho la chipani cha DPP kamba koti mu 2022, chipanichi chinali chitakanilidwa kaleso pempho lofanana ndi lomwe akufuna kupeleka pano.

Koma Lachisanu sabata ino, oweruza milandu Mdeza, wakana pempho la a Nankhumwa loti khothi lisamve pempho la chipani cha DPP pa nkhani yofuna kuchotsa chiletso chomwe chikuwateteza kuchotsedwa pa udindo wawo m’nyumba ya malamulo.

Popereka chigamulo chake, oweruza milandu Mdeza, wanena kuti sakuvetsetsa mfundo zomwe a Nankhumwa anapeleka pomwe ankaletsa bwalo la milandu kumva pempho la chipani cha DPP ndipo ati nkofunika kuti chipanichi chipatsidwe mwayi opereka pempho lake.

“Ngati pali chilichonse, mwina mfundo zimenezo zidzaperekedwe pa nthawi yakumva pempho la chipani cha DPP lofuna kuchotsa chiletso,” yatelo mbali ina ya chigamulo cha oweruza milandu Mdeza. 

Zatelemu, bwalo la milanduli likhazikitsa tsiku loti lidzamve pempho la chipani cha DPP pomwe chikufuna kuchotsa chiletso chomwe a Nankhumwa anatenga chowateteza kuchotsedwa pa udindo wa utsogoleri wa zipani zotsutsa boma m’nyumba ya malamulo.

Izi zikudza pomweso bwalo la milandu lakana ma pempho angapo omwe a Nankhumwa akhala akupeleka potsatira kuchotsedwa kwawo pa udindo komaso m’chipani cha DPP pa nkhani yosasunga mwambo.

Malipoti osatsimikizika akusonyeza kuti mkuluyu yemwe anali wa chiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha DPP mchigawo chakumwera, ali mkati mofuna kuyambitsa chipani chake pomwe akufuna kudzapikisana nawo pa udindo wa mtsogoleri wa dziko lino pa zisankho zomwe zilipo chaka cha mawa. 

Advertisement