A Chakwera ati Chitani Ulimi musadzimve u Big

Advertisement

Mtsogoleri wa dziko lino, Lazarus Chakwera, walimbikitsa a Malawi onse kuti asangodalira ntchito za mu ofesi koma adzichitanso ulimi komanso kusatsa malonda a zolima ponena kuti dziko la Malawi liri ndi chuma chochuluka mu ulimi.

Potsekulira sabata ya chionetselo cha za ulimi ku Bingu International Convention Centre (BICC) mu Mzinda wa Lilongwe, a Chakwera ati dziko la Malawi liri ndi zinthu zochuluka zomwe anthu ambiri amasilira atakhala nazo ndipo mkofunika kudzisatsa.

Mtsogoleri wa dziko linoyu wati aMalawi asayabwidwe ndi kukamba zabwino za dziko lake ndipo wati anthu apewe kufalitsa zoyipa za dziko lino zomwe  ena amalimbirapo mtima kupitiliza kuyipitsa mbiri ya dziko lino ndipo apempha anthu agwiritse ntchito luso lofalitsalo pa zabwino zomwe anthu sangazipeze kwina kulikonse.

“Tidziyamba ndife a Malawi kuipatsa moto Malawi, tidziyamba ndife kunenelela malonda a ku Malawi”

A Chakwera ati iwo akulimbikitsa ulimi wa minda ikulu ikulu, ulimi wa mnthilira  pakati pa achinyamata, amayi komanso magulu  kuti adzilima zochuluka za maonekedwe abwino kuti malonda asavute ponena kuti izi ndizo zobweretsa chuma komanso kutukula Malawi. 

Mmawu awo, Nduna ya Zamalimidwe a  Sam Kawale, ati ulimi ndi omwe ukuchita kwakukulu popititsa patsogolo chuma cha dziko lino mothamangira maso mphenya a Malawi 2063.

A Kawale ati mbali ya za ulimi ikubweletsa anthu akunja kulowetsa ndalama ku ulimi zomwe zikubweretsa chuma chochuluka kuphatikiza ndalama zakunja, kulemba ntchito anthu ochuluka.

Ndunayi yati, unduna wa za ulimi ukulowa ku ulimi wa makono kuti alimi azichepetsa zolowetsa ku ulimi ndi kupeza phindu lambiri kuphatikiza kupezelatu misika ya ogula zokolora.

Advertisement