Samalani chakudya, kuli njala- Joyce Banda

Advertisement

Mtsogoleri wakale wa dziko lino, Joyce Banda, walangiza mzika za dziko lino kusamala chimanga kamba ka njala yoopsa yomwe iyale mphasa chaka chino chifukwa cha kusintha kwa nyengo.

A Banda ayankhula izi Lachitatu ku Domasi komwe  amapereka chakudya, zikwama komaso kukhazikitsa ntchito yokonzanso zinthu zina ndi zina pa Gala pulayimale sukulu ndipo ati pakufunika machawi ogonjetsa vuto la njala m’dziko muno.

Pa nkhani yopititsa patsogolo maphunziro a ana, iwo anati sukulu yawo ya Joyce Banda Foundation ili patsogolo kukwanilitsa izi.

Mau ake, ophunzira wa STD 8 pa Gala pulayimale sukulu yemwe ali ndi vuto lorephera kuyenda,  Francis Gerald wayamikira mai Banda kamba ka njinga yomwe walandira ndipo wati izi  zimulimbikitsa kuti akhonze bwino mayeso a std 8.

Advertisement