Alimi muyenera kulondoloza fodya wanu kuti ena asalemelere ndi umbava otibera -atero a Chakwera

Advertisement

President wa dziko lino, a Lazarus Chakwera, ati alimi akuyenera kulondoloza fodya wawo moyenera cholinga choti ena asalemere powabera alimiwa potengera kuti ulimi wa fodya umafunika chidwi komanso kulondoloza chilichonse mu nthawi yoyenera.

A Chakwera anena izi pa msonkhano omwe anapangitsa pa sukulu ya pulayimale ya Vivya kwa mfumu yaikulu Njombwa ku Kasungu pomwe amatsegurira malonda a fodya ku msika wa Chinkhoma.

A Chakwera ati palinso ena omwe akulemera ndi ulimi wafodya pogwiritsa ntchito ana achichepere, zomwe zili zoletsedwa m’malamulo a dziko lino ndipo ati aliyense opezeka akuchita mchitidwe oterewu, akuyenera kuti anenezedwe kwa apolisi kuti mlimi oteroyo amunjate.

Mtsogoleri wa dziko linoyu anawonjezera ponena kuti aliyense atha kupindula ndi ulimi ngati angatsatire malamulo komanso ngati angakhale mlonda wa nzake ndi cholinga  chothana ndi umphawi omwe wamanga nthenje m’dziko lino.

“Tonse tikudziwa kuti a Ngwazi, omwe kwawo kunali ku Kasungu konkuno, anatiphunzitsa kuti chuma chili munthaka, ndipo palibe boma m’Malawi muno linadalitsidwa ndi chuma chanthaka yaulimi ngati Kasungu. Koma chodabwitsa n’choti ena konkuno alibe malo olimila chakudya chao chifukwa ambiri anagulitsagulitsa minda yao kwa anthu ndi makampani akutauni.

“Ndiye nthawi yokolora ngati ino, upeza ku Kasungu kuno kuli minda ikulu ikulu ya chimanga chowilira, koma chonsecho anthu ena ku Kasungu konkuno amangochisilira chimangacho podziwa kuti sichawo chifukwa iwo samalima minda yao anagulitsa. Tiyeni tizikhalako serious ndi chuma chathu,” a Chakwera anatero.

Iwo ati anthu atha kupeza njira zobwereketsera minda yawo kwa ena komanso yowonetsetsa kuti  ndime yokolora chakudya chawo alinayo ncholinga choti azipindura mbali zonse ziwiri komanso apitilize kukhala eni minda .

Poyankhurapo, wapampando wa bodi ya Tobacco Commission (TC), a  Dr. Godfrey Chapola, ati pali anthu ena omwe akugulitsa fodya kwa ma Kampani omwe alibe ziphatso zoyenerera ndipo amatumiza fodya amaneyo maiko akunja mosatsatira malamuro zomwe zimapangitsa kuti malonda a fodya asapite patsogolo ndipo ati mchitidwe umenewu ufufuzidwe ncholinga choti fodya wa dziko lino adzikugulitsidwa m’dziko muno kuti chuma chipite patsogolo.

A Chapola atinso iwo anaona chanzeru kuti athandizepo anthu omwe akhunzidwa ndi kusefukira kwa madzi  m’ma boma ena a m’dziko muno potengeranso kuti ena mwa anthuwo ndi alimi kotero athandiza ndi ndalama zokwana 10 Million Kwacha ngati njira imodzi yothandiza boma pa ntchito yomwe akugwira pothandiza anthu omwe awonekeredwa ngoziyi.

Chaka chino, fodya yemwe akuyembekezedwa kugulitsidwa pa msika ndi olemera makilogaramu 140 Million. Chaka chatha, fodya olemera makilogaramu 121 Million ndi yemwe anagulitsidwa. 

Kupatura kutsegulira malonda a msika wa fodya , a president Lazarus Chakwera anatsegurira ma ofesi atsopano a Tobacco Commission omwe amangidwa ndi ndalama zokwana 190 Million Kwacha komanso  kukayendera nyumba zomwe akumangira a silikali aku Kasungu Engineering Battalion kwa mfumu yaikulu Njombwa.

Advertisement