Ochita malonda mumsika waukulu wa Zomba sakukondwa ndikukwera kwa chiphaso

Advertisement

Anthu ochita malonda mumsika waukulu wa Zomba ati sakukondwera ndizomwe achita akulu akulu akhonsolo ya mzindawu pokweza mtengo wachiphaso kuchoka pa K200 kufika pa K300 patsiku.

Wapampando wa anthu ochita malondawa a Ayatu Chidothe ati Khonsolo ya mzinda wa Zomba yafulumira kukwedza mtengo wodulira chiphasochi popeza masiku ano zinthu sizikuyenda ndipo ochita malonda sakuchita phindu lirilonse, mmalo mwake, akukakamizika kumatenga ndalama kunyumba kumakadulira chiphaso popeza ena amatha sabata asadagulitse kanthu.

A Chidothe ati ochita malonda mumsika waukulu wa Zomba amawononga ndalama zambiri patsiku popeza ndalama zina amakalipira kuchimbudzi akafuna kuti akadzithandize komanso amakagula madzi popeza akhonsolo adapereka zimbudzi komanso madzi kwa anthu kuti adzilipilitsa munthu akafuna kugwiritsa ntchito.

Iwo adadandaulanso kuti khonsoloyi ikulephera kusamalira msikawu popeza zinyalala komanso zoyipa zimangotayidwa m’malo osayenera zomwe zimayika pachiwopsezo chodwala matenda otsekula mimba kwa anthu ochita malondawa. 

“Khonsolo ikulephera kuchotsa anthu omwe amachita malonda malo osayenera (illegal vending) omwe samalipira chiphaso ndipo ife timalephera kugulitsa chifukwa cha anthu amenewa komanso timalephera kupeza ndalama zolipilira chiphasochi,” anatero a Chidothe.

Poyankhulanso ndi Malawi24, mai wina yemwe sadafune kumutchula dzina adati zomwe akuchita akulu akulu akhonsolo ya mzinda wa Zomba ndikufuna kupondereza ufulu wa anthu ochita malonda popeza adakweza mtengo wachiphaso asadakambirane nawo ochita malondawo.

Iwo adati Khonsolo imangokomedwa kutolera ndalama koma ndalamazi sizimagwira ntchito yake yosamalira msikawu ndiponso adapempha kuti achotse onse omwe amayendayenda ndimalonda minseu.

Khonsolo ya mzindawu idalengeza kuti yakweza mtengo wodulira chiphaso mimsika yake yonse kuchoka pa K200 kufika pa K300 kwacha kuyambira pa 1 April.

Advertisement