Itaphulika nkhani yokhudza mchitidwe wa aphunzitsi a sukulu ya ukachenjede ya Mzuzu University kugonana ndi ophunzira pofuna kusinthana ndi malikisi kuti akhonze, sukuluyi tsopano yayamba kufufuza kuti apeze yemwedi akuchiti izi.
Sukuluyi yatsindika izi mu chikalata chake kuti ikulondola mwa chidwi nkhani imene yafala mu masamba a mchezo yokhudza aphunzitsi ena pa sukuluyi omwe amauza ophunzira akazi kuti agone nawo pofuna kuti achite bwino pa maphunziro awo zomwe zili zophwanya malamulo.
Sukuluyi, kudzera mu kalatayi ,yatinso akuluakulu a sukuluyi sanapatsidwe mwayi kuti ayankhulepo zokhudza nkhaniyi, ndipo ati mpofunika kupeza chilungamo kuti lamulo ligwire ntchito kwa anthu amene akukhudzidwa.
Kalatayi yatinso sukuluyi inakhazikitsa ndondomeko zosiyanasiyana pofuna kuthana ndi mchitidwe wakatangale ndi ziphuphu za mtundu wina uliwonse ponena kuti pakadali pano sukuluyi ikugwira ntchito ndi bungwe lolimbana ndikatangale komanso ziphuphu la Anti-corruption Bureau (ACB).
Sabata yangothayi, masamba a mchezo adafala ndi nkhani yakuti mwana wina wa sukuluyi adadandaula za kukakamizidwa kuti agone ndi mmodzi mwa aphunzitsiwa pofuna kusinthana ndi malikisi mcholinga choti akhonze mayeso, ndipo anthu popelekera ndemanga ati khalidwe la ngati ili likuchitika mu sukulu zambiri za ukachenjede za boma mdziko muno.