Mbava zowombera mwini nyumba zagwidwa ku Blantyre

Advertisement

 A bambo atatu ku Soche mu nzinda wa Blantyre, ali manja mwa apolisi kamba kowombera ndi mfuti mwini nyumba yomwe anapita kukaba.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi wachiwiri kwa ofalitsa nkhani pa polisi ya Soche a Hopeness Potani omwe azindikira mbavazi ngati a Madalitso Mthupi azaka 34, Mike Davie a zaka 28 komaso a Gift John a zaka 19.

A Potani ati kumayambiliro kwa sabata ino, anthu oganizilidwawa anapita kukachita zachiwembuzi ku kunyumba ya bambo Alex Makanjira yomwe ili ku m’mawa kwa dera la Soche munzindawu.

Ofalitsa nkhaniyu wati, atatuwa atafika ku nyumbayi, anawombera mwini nyumbayi pamimba ndikuba kanena ya ntundu wa plasma, makina a computer, ma foni a m’manja awiri ndi ndalama zokwana K100,000.

Atatelo, anthu akubawa, anathawa kuwasiya bambo Makanjira ali mu ululu osasimbika ndipo agwidwa potsatira kafufuku yemwe apolisi anakhazikitsa atalandira nkhaniyi.

Atatuwa atagwidwa, apezeka ndi mfuti ya mtundu wa AK47 yomwe akuti ndi yomwe adagwiritsa nchito pa chiwembuchi komaso kanema yomwe anabayo.

Apolisi ati a Mthupi, a Davie ndi a John, onse amachokera m’boma la Nsanje.

Advertisement