Mayi athawa atapha mamuna wake pomukoka katundu

Advertisement
Malawi 24 news logo

Mayi wina yemwe dzina lake silikudziwika Boma la Zomba wathawa atapha mamuna wake pomukoka malo obisika.

Wofalitsa nkhani za apolisi Boma la Zomba, Sub Inspector Patricia Sipiliano watsimikidza zankhaniyi poyankhula ndi Malawi24.

Sub Inspector Sipiliano wati izi zachitika mmudzi mwa Makanjira mdera ya Mfumu yayikulu Chikowi Boma la Zomba ndipo wati  bamboyu dzina lake ndi Valentine Nazombe.

Sub Inspector Sipiliano atsimikiza za nkhaniyi.

Iye wati a Nazombe adapedzeka atafa koma katundu wao (malo obisika) atawonongeka.

Wofalitsa nkhaniyu wati pakadali pano apolisi akufuna funa mayiyu ndipo akapezeka amutsekulira mulandu wakupha.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.