Bwalo lamilandu ku Zomba lidzapereka chigamulo chake pa 10 May pa mulandu wa Bon Kalindo

Advertisement
Bon Kalindo is being tried for leading protests which ended with violence

Bwalo la Principal Resident Magistrate ku Zomba likuyembekezeka kudzapereka chigamulo chake pa 10 May kwa mkulu wa Bungwe la Malawi First a Bon Kalindo pamulandu womwe akumuyimba woyambitsa chisokonezo paziwonetsero zomwe adachititsa mu mzinda wa Zomba pa 23 November chaka chatha.

A Kalindo adabweretsa mboni zisanu ndipo mboni ziwiri zatsiliza kuperekera umboni wao Lolemba mamawa ndipo mboni yotsiliza yomwe ndi Mai Chisomo Chinyama idawuza bwalo kuti anthu omwe adayambitsa chisokonedzo pa nthawi ya ziwonetsero adachita mokufuna kwao popeza a Bon Kalindo adaneneratu kuti pasapezeke munthu oyambitsa zipolowe.

Poyankhulapo, Lawyer yemwe akuyimira a Kalindo a Timothy Chirwa adati ndiwokhutitsidwa ndi momwe mboni zawo zaperekera umboni mubwalo lamilandu ndipo chatsala ndikuti oweredza apereke chigamulo chake.

Principal Resident Magistrate Martin Chipofya yemwe akuzenga mulanduwu wayamba wayimitsa mulanduwu mpaka pa 10 May nthawi ya 2 koloko masana pomwe adzapereke chigamulo chake ndipo wauza mbali zonse ziwiri kuti zikhale zitapereka ma submission awo pofika pa 4 April.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.