Unduna wati alimi asagulitse chimanga chinakali m’munda

Advertisement

Pomwe pali chiopsezo cha njala yadzaoneni, unduna wa Zamalimidwe walangiza anthu kuti ayesetse kulima chimanga komaso mbewu zina m’madimba ndipo wachenjeza kuti uthana ndi mchitidwe oberana komaso kugulitsa chimanga ndi mbewu zina zisanakhwimitsitse komanso zinakali m’munda.

Izi ndi malingana ndi kalata yomwe undunawu watulutsa yomwe wasainira ndi Dickxie Kampani yemwe ndi mlembi mu unduna wa zamalimidwewu, yomwe yati kutsatira ng’amba komanso kusefukira kwa madzi zomwe zakhudza madera ambiri m’dziko muno, chaka chino zokolola zikuyembekezeka kukhala zocheperako.

Undunawu wati ndizodandaulitsa kuti pomwe pali chiopsezo cha njalachi, mchitidwe oberana komaso kugulitsana mbewu zosiyanasiyana zisanakhwimitsitse, zinakali m’munda wachuluka kwambiri pakati pa anthu zomwe akuti zitha kuwonjezera chiopsezo cha njala.

“Ngakhale zinthu zili chomwechi, ndi zachisoni kuti Undunawu wapezanso kuti kukuchitika umbava komanso malonda a chimanga chachiwisi nthawi yake yokolola isanafike. Izi zikuika dziko lino pa chiopsezo chachikulu cha kuchepa kwa chakudya.

“Unduna wa Zamalimidwe ukuchenjeza onse ochita malonda ogula ndi kugulitsa chimanga chikanali m’munda komanso omwe akumabera alimi kuti akagwidwa lamulo lidzagwira ntchito,” yatelo mbali ina ya kalata ya undunawu.

Undunawu wapitilira ndikufotokoza kuti pofuna kuonetsetsa kuti chakudya chikupezeka ngakhale dziko lino lakhudzidwa ndi ng’amba ndi kusefukira kwa madzi, alimi asagulitse chimanga chawo chikanali m’munda komanso alime chimanga ndi mbewu zina m’madimba.

“Alimi akukumbutsidwa kusunga chimanga chokwanira banja lonse pa chaka (munthu m’modzi wamkulu amafunika matumba 4 a chimanga olemera makilogalamu 50 thumba lirilonse pa chaka). Undunawu ukulimbikitsanso alimi kuchita ulimi wa chimanga wa m’madimba komanso kubzala mbewu zina monga mbatata, chinangwa ndi nseula.

“Onse omwe ali ndi kuthekera kolima m’malo amene amakhala ndi chinyontho komanso omwe ali ndi kuthekera kochita ulimi wa m’nthilira akulimbikitsidwa,” yatelo so mbali ina ya kalata kuchokera ku unduna wa malimidwewu.

Unduna wa Zamalimidwewu wapempha alimi ndi anthu onse okhudzidwa kuti atsatire malangizowa pofuna kuteteza anthu m’dziko muno ku mavuto akuchepa kwa chakudya.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.