Tikutumiza chimanga chochepa dala pofuna kuteteza ku mbava – Sam Kawale

Advertisement
Sam Kawale Minister of Agriculture

Nduna yowona za malimidwe a Sam Kawale ati boma likhala likupitiliza kutumiza chimanga chimene likusunga mu nkhokwe zake ku misika ya ADMARC m’dziko muno ngakhale anthu pakali pano ayamba kukolola chimanga m’minda yawo madela ena.

A Kawale amayankhula izi m’nyumba ya malamulo pamene Phungu wa nyumba ya malamulo ku m’mawa kwa boma la Chiradzulu anafunsa za chifukwa chimene boma likusunga chimanga mu nkhokwe zake pamene anthu ena m’madela akufa ndi njala komanso kuti chimangachi chikanachititsa mitengo ya ma venda kutsika.

A Kawale ati boma Kudzela ku unduna wawo ukutumiza Chimanga chochepa dala kufuna kuchepetsa mchitidwe wa umbava m’misika ya ADMARC zomwe zimadza nthawi zina chifukwa chokanganilana kugula pena mwa dala kumene.

A Kawale ati kukhala ndi Chimanga mu nkhokwe pakadali pano sikukutanthawuza kuti chimangachi sichipita ku misika ayi. Iwo ati malinga ndi zomwe anafotokoza mtsogoleri wa dziko m’nyumba ya malamulo, chimangachi chikhala chikupitabe ku misika kufikira July.

A Kawale ati pamene ntchito yogawa chimanga ikupitilila, maboma ena monga Blantyre, Chiradzulu, Lilongwe, Machinga, Mangochi, Mulanje, Mzimba , Thyolo, Dowa, Karonga, Ntchisi ndi Chitipa akhala akulandila Ufa omwe udagulidwa ndi thandizo lochokera ku Banki yayikulu pa dziko lonse (World Bank).

Advertisement