A Mutharika awapempha aganize bwino pa lingalilo lawo lofuna kuimanso

Advertisement

A Undule Mwakasungula omwe ndi m’modzi mwa anthu amene amayankhulapo pa ndale ati a Peter Mutharika akuyenera aganize bwino pa lingalilo lawo lofuna kudzapikisana nawo pa mpando wa upulezidenti.

A Mwakasungula ati ngakhale a Mutharika akukhulupira kuti utsogoleri wawo ndi ofunikira, pali zolepheretsa zambiri kuti adzawineso pa chisankho cha 2025.

“Zaka zawo, umunthu komaso nkhani za katangale zomwe iwo ndi boma lawo amachita a Malawi akukumbukirabe ndipo izi ndi zina zimene zizalepheretse kuwina pa zisankho.

“Choncho akuyenera aganizile bwino ngati utsogoleri wawo udzakwaniritse zofuna a Malawi,” anatero a Mwakasungula.

Katswiriyu anapitiriza kunena kuti a Mutharika akuyenera kumvetsetsa kuti kuliso moyo wina ukachoka pa mpando wa upulezidenti ndipo ali ndi kuthekera kosintha zinthu m’dziko muno pamene iwo ali pulezidenti opuma.

Mukuyankhula kwa a Mutharika pamene anali ndi nsonkhano wa atolankhnai ku nyumba ya chifumu m’boma la Mangochi, anati ganizo lawo lofuna kuzapikisana nawo pa zisankho za 2025 ladza chifukwa cha mavuto amene a Malawi akukumana nawo kamba kosowa utsogoleri wabwino.

Advertisement