‘Amene anatha ndiamene anamwalira munthu samatha ali moyo’- watero Chipiliro Mwancheka

Advertisement

Oyimba Chipiliro Mwancheka wati iye sanathe ndipo atulutsa chimbale chatsopano chotchedwa ‘Ndabwera’ posachedwa.

Chimbale chatsopano chimene akuyembekezera kutulutsa muli nyimbo zokwanira khumi ndipo zonse wayimba yekha.

Nyimbo zisanu ndi zitatu wajambula yekha ku studio kwake pomwe ziwiri zajambulidwa ndi Viwe Chibwana, Dj Lobodo mothandizana ndi Banderous.

Mwancheka wanenanso kuti nyimbo za tsopanozi waphatikizamo makhirikhiri chifukwa ndi chamba chachingoni ndipo angoni amapezeka paliponse.

“Ndimayimba Makhirikhiri chifukwa ndinafuna kusiyana ndi anthu ena komaso ndimakonda zachikhalidwe moti mu chimbalechi mulinso tchopa komanso vimbuza,” anatero Mwamcheka.

Mukucheza kwathu Mwancheka anaunikiranso kuti mayimbidwe ku Malawi akusowekera m’gwirizano okwanira kuti tibooleze misika ya kunja.

Mwamcheka anadziwika mu chaka cha 2008 atatulutsa nyimbo yotchedwa ‘Ndibwera’ yomwe inayimbidwa mu chamba cha makhirikhiri cha ku Botswana

Mwanyimbo zina zotchuka zomwe anayimba ndi monga ‘Kadonaka’ yomwe anathandizana ndi Nepman komanso ‘Ndilekele’ yomwe anayimba yekha.

Mwamcheka anatsiliza kumema omutsatira ndi onse amakonda nyimbo zake kuti apitilize kumupanga sapoti chifukwa ulendo uno wabweretsa zokoma kuposa kale ndipo amva bwino ndinthu.

Advertisement