Dziko lino lili pa chiopsezo cholandiraso namondwe

Advertisement

Nthambi yowona za nyengo yati pali kuthekera koti namondwe yemwe akuyembekezeka kubadwa mnyanja ya m’chere ya India, akhoza kudzafika kapena kuyandikira kum’mwera kwa dziko lino.

Malinga ndi nthambiyi, Namondweyu sanabadwe koma akuyembekezeka kubadwa mu Nyanja ya Mchere ya India pakati pa mayiko a Madagascar ndi Mozambique pofika Lamulungu lino pa 10 March, 2024.

“Pali chiyembekezo chakuti Namondweyu akabadwa adzachuluka nyonga zake,” yatero nthambiyi.

Pakadali pano, nthambi yoona za nyengoyi yati Namondweyu sanabadwe ndipo njira imene angadzatenge sinadziwike kwenikweni.

Komabe nthambiyi yati pali kuthekera koti akhoza kufika kapena kuyandikira ndi kum’mwera kwa dziko lino.

Advertisement