Adzukulu amangilira njonda ziwili pamtengo ku manda a Kabwabwa

Advertisement

Adzukulu okumba manda amangilira anthu awili pamtengo kumanda a Kabwabwa kamba kotolera chipepeso cha maliro popanda chilolezo kuchokera kwa amfumu a ku Area 25B (Kabwabwa) munzinda wa Lilongwe.

Mayina a anthu awili omwe amangidwa pamtengowa ndi a Yusuf Steven komanso a Patrick Tambula.

Nkhani yonse ikuti mderali munachitika zovuta ndipo anyamatawa anayamba kusonkhanitsa chipepeso popanda kutenga chilolezo kwa amfumu amderali.

Anthu anatutumuka kuona anyamata awiliwa akutolera chipepeso chonsecho koma sakhala mudelaro. Apa eni mudzi anayamba kuwatsatira mpaka kuwagwira kuti afotokoze bwino.

Apa anyamatawa anangokhala chete kusowa choyankha pozikindikira kuti fisi akagwera mbuna salankhula.

Kenako adzukulu anamangilira anyamata awiliwa pamtengo kumanda a Kabwabwa uku akudikira nyakwawa yaderalo kuti ipereke chigamulo chake pankhaniyi.

Advertisement