Mlatho wakokoloka ndi madzi ku Kasungu

Advertisement

Mayendedwe akhala ovutirapo pamene mlatho wapamtsinje wa Chitete omwe uli pafupi ndi sukulu ya sekondale yoyendera ya Boma Community Day Secondary school (C.D.S.S) mumanisipalite ya Kasungu wakokoloka ndi madzi kutsatira mvula yamphamvu yomwe yagwa kuyambira dzulo.

Malipoti akuti mlathowu udayamba kukokoloka m’mwezi watha wa January ndipo mvula yomwe yakhala ikugwa mtauniyi yamalizitsa kambali komwe kadatsala.

Pakadali pano kuwoloka pa mtsinjewu ndikovuta ndipo anthu ozungulira derali akuyenera kuwoloka pogwilitsa ntchito mlatho wa Kandodo kuti apite ku tsidya lina.

A Heese Nyangu omwe ndi mfumu yamanisipalite ya Kasungu ati khonsolo ya bomali yayika kale padera ndalama zokonzera mulathowu kotero ntchito yokonza mulathowu iyamba m’mwezi wa April chaka chino.

Advertisement