Mtambo wadzudzula kumenyana pa ndale

Advertisement
Timothy Mtambo Malawi

A Timothy Mtambo omwe ndi mtsogoleri wa bungwe la Citizens for Transformation (CFT) ati mchitidwe wochita ziwawa pa nkhani za ndale ukuyenera utheletu mdziko muno.

Izi ndi malingana ndi kalata yomwe bungwe la CFT latulutsa yomwe wasainira ndi Mtambo, yemwe wadzudzula mtopola omwe anthu ana anachita Loweluka lapitali pomwe anasokoneza komaso kuvulaza otsatira chipani cha Democratic Progressive (DPP) nthawi yomwe chipanichi chimafuna kukhala ndi zochitika munzinda wa Lilongwe.

A Mtambo ati zomwe zinachitika ku Lilongwe-zi komaso zipwilikiti zina zomwe zinachitika posachedwapa ku Zomba ndi ku Blantyre, ndizosayenela mdziko muno makamaka pa nthawi ino pomwe aliyese maso ake akulunjika ku zisankho za patatu chaka cha mawa chino.

A Mtambo kudzera mu kalatayi ati pamene a Malawi adasankha ulamuliro wa zipani zambiri pa “referendum” mu 1993, chinali chivomelezo choti pazikhala kulolerana pa ndale, ndipo wanenetsa kuti anthu omwe akukolezera mchitidwe wa ziwawa pa dzina la ndale, alibe tsogolo.

“Bungwe la Citizens for Transformation (CFT) laona monyansidwa ziwawa zomwe zachitika pa misonkhano ingapo; wina ku Zomba ndi Blantyre m’masabata apitawa, komanso pa 24 February 2024 ku Lilongwe. Zochitika zonyansazi siziyenera kuwonedwa ngati zochitika zosiyana komanso zazing’ono zomwe zimachitidwa ndi anthu ankhanza osakondwa koma ziwopsezo zazikulu zachitetezo cha boma komanso chiwopsezo ku ulamuliro wa zipani zambiri yomwe tinsupeza movutikira.

“CFT ikufuna kukumbutsa omwe akuthandiza komanso akulimbikitsa ziwawa za ndale ndi mawu achidani m’Malawi, kuti alibe tsogolo la ndale kapena m’nthawi yamakono ngati ino pomwe magulu osiyanasiyana amachitira zinthu limodzi ndicholinga chofuna kupititsa pa tsogolo mfundo za chitukuko,” atelo a Mtambo kudzera mu kalata ya CFT.

Mkuluyu yemwe naye wakhala akutsogolera zionetsero boma la Tonse lisanasankhidwe kulamulira dziko lino, wati bungwe lawo la CFT silikhala chete ndikumayang’anira dziko lino likusandutsidwa la chisawawa pa zifukwa za zochitika za ndale ndi nzika zachinyengo.

Iwo akumbutsanso a Malawi onse kuti udindo wolemekeza malamulo a dziko lino omwe amapereka ufulu wa ndale ndi ufulu kwa akuluakulu a boma, ndale, zipani za ndale, otsatira awo, ndi nzika zonse, uli m’manja mwa munthu aliyese ndipo apempha unduna wa za chitetezo kuti mwa nsanga nsanga unjate onse obweretsa chisokonezo pa zifukwa za ndale.

“Tikupemphanso Unduna wa Zachitetezo cha Dziko kuti ukhazikitse mtendere, malamulo, ndi bata poweruza mwachangu onse oyambitsa ziwawa za ndale ndi mawu achidani, makamaka pano pamene tikuyandikira chisankho chapatatu cha 2025. Zipolowe za ndale ndi chisonyezo cha mantha komanso ndi khalidwe lopanda pake. Tiyeni tonse tikane kuchita ndale za zipolowe komanso zosatukuka,” yateloso mbali ina ya kalatayi.

A Mtambo anatsendera ndi kunena kuti bungwe la CFT, lidzakhalabe lodzipeleka kulimbikitsa mfundo zikuluzikulu za ufulu, kudalirana, kulimbikitsa chuma cha dziko, mgwirizano wa dziko kwa onse, kudzipereka ndi kukonda dziko lawo kwa a Malawi onse.

Advertisement