Bushiri wasayinira mgwirizano ndi katsiwiri wa ma filimu  Nkem Owoh wa dziko la Nigeria

Advertisement
Shepherd Bushiri with Nigerian actor Nkem Owoh in Lilongwe Malawi

Mneneri Shepherd Bushiri kudzera pansi pa bungwe la Shepherd Bushiri Foundation (SBF) wasainirana mgwirizano ndi katakwe pa nkhani yochita ma filimu wa m’dziko la Nigeria, Nkem Owoh, lamulungu lapitali mu mzinda wa Lilongwe ngati njira imodzi yopititsa patsogolo luso lochita  mafilimu m’dziko muno.

Uthenga omwe walemba ndi oyankhulira a Bushiri, Aubrey Kusakala, wati cholinga cha mgwirizanowu ndi kupititsa patsogolo luso lochita ma filimu m’dziko muno ndipo izi zithandizira kuti achinyamata amene ali ndi luso lotere m’dziko muno.

Mu mau ake, mneneri Shepherd Bushiri wati akuyembekezera mgwirizano komanso umodzi pakati pa anthu ochita ma filimu m’dziko muno ndi m’dziko la Nigeria.

Iye anati: “Ndimakhala ndi chikhulupiriro kuti luso  tili nalo ife a Malawi koma timasowa kupeza njira yoti dziko la pansi litidziwe koma ndi mgwirizano uwu zithandizira kukweza lusoli, choncho tikuyenera kugwirana manja kuti izi zitheke”.

Malingana ndi a Bushiri, mgwirizanowu ukuyembekezeka kukhala ndi magulu awiri amene atulutse kanema oyamba kuyambira mwezi wa April chaka chino ndipo posachedwa atulutsa ndondomeko ya m’mene anthu  amene angakonde kutenga nawo mbali  mu kanemayi alemberetsere.

Bushiri kudzera mu bungwe la Bushiri Foundation komaso kampani yake yojambula njimbo ya Major one records wakhala akutukula komaso kupititsa patsogolo luso la oimba osiyanasiyana dziko muno.

Wolemba : Peter Mavuto

Advertisement

One Comment

Comments are closed.