Phungu wa Chikwawa West wathokoza boma chifukwa chofuna kumanga nsewu wa Chapananga

Advertisement

Phungu wa mdera la Chikwawa West a Susan Dossi athokoza boma la a Lazarus Chakwera chifukwa chofuna kumanga nsewu wa Chapananga omwe wakhala nthawi yayitali utawonongeka.

A Dossi awuza Malawi24 potsatira zomwe adayankhula mtsogoleri wadziko lino a Chakwera ku mtundu wa a Malawi ku nyumba yamalamulo pankhani yofuna kukonza nsewu wa Chapananga omwe adati ukadzatha udzidzatchedwa Sidik Mia Highway.

‘Zomwe adayankhula a Chakwera zikupereka chiyembekezo kwa a Malawi’- Dossi

Iye wati anthu a m’boma la Chikwawa West akhala akuvutika mayendedwe kwa nthawi yayitali chifukwa chakuvuta kwa nsewu wa Chapananga ndipo adati kukonzedwa kwa nsewu umenewu kudzapangitsa kuti anthu a mdera lake adzamukumbukire Chakwera moyo wao onse.

Iwo anati atsogoleri omwe akhala akulamulira m’mbuyomu ankangolonjeza ikafika nthawi yamisonkhano yokopa anthu koma malonjezo awo samawakwanilitsa.

Phunguyu wati zomwe adayankhula a Chakwera zikupereka chiyembekezo kwa anthu popeza adakambamo nkhani zachitukuko zambiri ndipo iye wadzudzula anthu ena omwe akunyozetsa zomwe adayankhula a Chakwera ponena kuti kumeneku ndikusayamika.

A Dossi adati iwo ngati phungu wakunyumba yamalamulo pamodzi ndi anthu aku Chikwawa West ali okonzeka kugwira ntchito zachitukuko ndi mtsogoleri wadziko linoyu chifukwa pakali pano sinthawi yopanga ndale koma chitukuko.

“Mtsogoleri wa dziko amakhala m’modzi ndiye tiyeni tiwapatse mpata a Chakwera kuti agwire ntchito yawo yotukula m’madera mwathu chifukwa zomwe adayankhula kunyumba yamalamulo muli mfundo zambiri zachitukuko ndipo zapereka chiyembekezo kwa a Malawi,” adatero a Susan Dossi.

Pamenepa iwo adati nsewu umenewu ukatheka udzakhala ofunikira kwambiri chifukwa wafika ku malire a Mozambique komanso walumikiza maboma a Chikwawa ndi Mwanza.

Nsewu wa Chikwawa udzathandizanso kampani ya Ilovo kuti azizatumiza shuga mosavuta ku Mwanza ndi ku Mozambique komanso udzathandidza alimi kuti zokolola zawo zidzidzadutsa mosavuta

Advertisement