Ras Chikomeni David Kadelele Chirwa yemwe amadziwika bwino ndi dzina loti Ras Chikomeni, ati ndi okonzeka kuyimanso ngati m’tsogoleri wa dziko lino pa zisankho za patatu mu 2025.
A Chikomeni anali ndi chidwi choyima pa zisankho za 2019, koma izi sizidatheke kamba kosowekera ndalama ya chikole cha zisankho yokwana 2 Million Kwacha, komanso osayinira 19 ochokera m’maboma 28 m’dziko muno ngati mboni.
Ngakhale zidawavuta mu zisankho zapitazi, iwo anena kuti anali ndi masomphenya otukula miyoyo ya a Malawi .
“Ngati anthu angaonetse chidwi chondithandiza kuti ndiyimenso ndili okonzeka kuzaonetsetsa kuti miyoyo ya a Malawi ili bwino muzonse makamaka zachuma, maphunzilo ndinso za umoyo.” adatero a Chikomeni.
Iwo atsimikiza kunena kuti palibe ubale ulionse ndi chipani cha DPP chichokereni chipanichi m’boma.
A Chikomeni omwe ali ndi zaka 46 zakubadwa anandaula kuti boma la Tonse Alliance lalephera kukwanilitsa zomwe linalonjeza zolemba ntchito anthu 1 million komanso kuthetsa katangale.
Iwo adapitiriza kunena kuti khomo ndilotseguka kwa m’malawi aliyense amene akufuna kugwila nawo ntchito mwachilungamo monga anachitila ndi a pulezidenti akale a Peter Mutharika mu 2019, komanso a pulezidenti Lazarus Chakwera ndi achiwiri awo a Saulos Chilima mu chaka cha 2020.
“Chimene ine ndimadandaula ndi chakuti akuluakulu ena amafuna azitigwiritsa ntchito achinyamata kenako kuzatisiya akapeza zabwino zimene akufuna,” anadandaula a Chikomeni.
Iwo adati ngati anthu akufuna kuti mayi awo asadzakhale wachiwiri wawo, Iwo ndiokonzeka kutero.
“Ngati anthu atafuna kuti mayi anga asakhale running mate palibe vuto chifukwa alipo ena omwe ndimawaona kuti athanso kugwila nane ntchito bwinobwino.” iwo adaonjezera.
Pakadali pano Ras Chikomeni ali kumunda (Farm) yomwe adasiilidwa ndi bambo awo ku Chamalaza ku Mzuzu, ndipo akuchita ulimi osiyanasiyana ndikusamala za chilengedwe.