Msika wa Matchansi ku Lilongwe ukosowekera ukhondo

Advertisement

Msika wa Matchansi ku Lilongwe, omwe umadziwika bwino ndi malonda a chakumwa choledzeretsa ndi nyama ya pachiwaya, ukuika pa chiopsezo cha matenda kwa anthu ogula ndi ogulitsa kamba koti dzala lotaila dzinyalala lidayandikana ndi malo ootchela mang’ina komanso bala.

Ntchito yosamalira msika imakhala m’manja mwa akuluakulu amene anasankhidwa kupyolera muma voti omwe anthu ochita malonda anasankha kuti aziyendesa zichitochito za msikawu.

Kuchokera mwezi wa novembala chaka chatha anthu ochita malonda mumsikawu akhala akudandaula za kusowekera kwa ukhondo umene umachitika pa malo otayira zinyalalawa kamba kakuchedwa kwa galimoto yozatenga kuchokera ku khonsolo.

Gift Mbetewa yemwe amadziwika ndi dzina loti Madinda, m’modzi mwa anthu ochita malonda mu msikawu watitsimikizira kuti chaka chatha galimoto lomwe limatenga zinyalala linatha mwezi onse wa disembala lisakugwira ntchito yake yochotsa zinyalala pa malowa.

“Ma kasitomala athu akumadandaula fungo komanso tili pa chiopsezo chodwala matenda okudza kamba kakusosowekera kwa ukhondo,” anatero Lameck Masina ogulitsa mowa mu msikawu.

Derali lomwe khansala wake ndi Juliana Kaduya, yemwenso ndi mfumu ya Lilongwe yopuma
tinayesa kuti tiyankhulane nawo zokhuza nkhaniyi koma zikumveka kuti sali mu dziko muno.

Khonsolo ya Mzinda wa Lilongwe imatolera ndalama zokwana 250 Kwacha ngati chiphaso kwa aliyense ochita malonda mumsikawu.

Yohane Kambere, wachiwiri kwa wa mkulu oyang’anira msikawu adatiuza kuti atatchaya lamya ku Khonsolo ya Mzinda wa Lilongwe adauzidwa kuti galimoto lotenga zinyalala lidaonongeka mwezi wa Disembala.

Adapitiriza kufotokoza kuti ngangakhale zili chomwechi mwezi wa Januwale galimoto linabwera kawiri kokha pano pakutha pafupifupi sabata zitatu.

Malowa aliso moyandikana ndi chimbudzi moti nthawi ya mvula ngati ino mphutsi zikumakhala yakaliyakali kuzungulira pa malowa.

Advertisement