Mfumu yaikulu ya angoni ku chigawo chakumpoto Inkosi Ya Makosi M’mbelwa Ya Chisanu yayamba yaimitsa kaye mafumu asanu kamba kothandizira kuwononga chilengwe.
Mfumu Mbelwa yayankhura izi pa mwambo wobzala mitengo womwe unachitikira pa sukulu ya pulayimale ya Luwelezi m’dera la Inkosi Mabilabo.
Mafumu omwe awayimitsawa ndi monga a Chihema, Kasankha, a Chiziyani, a Mchitilare komanso a Muyombe.
Mu mawu ake, Mfumuyi yati yachosa mafumu asanuwa kamba kokuti Madera omwe iwo akuyang’anira mitengo yachilengedwe yapululuka.
”Sindingalolere kuti mtchitidwe umenewu wowononga mitengo uzipitilira ndipo pano ndikulamula kuti mafumuwa ayambe kaye aima kugwira ntchito za ufumu , kuyambira panopa, ndipo ndikulamulaso kuti akuyenera kubwera ku ofesi kwanga pompano,” inatero Mfumuyo.
Mfumuyi inadzudzulanso akuluakulu wong’anira za nkhalango kuti ndiwo akukolezera mtchitidwe wowononga mitengo.
Iwo anapereka chisanzo chakuti adapeza munthu atanyamula mitengo yambiri mugalimoto lake koma, atamuyimitsa ndikumufunsa, munthuyo anatulutsa pepala la chilolezo (GR) yomwe imasonyeza kuti muthuyo waloledwa kudula mitengo.
Ndipo anaonjezera kuti ngati boma silichitapo kanthu iyo ndiyokonzeka kulanda nkhalango zonse zomwe zili m’manja mwa boma ponena kuti boma lalephera kuteteza nkhalangozo.
Pamwambowu panali akulu akulu monga Bwana Mkubwa wa Boma la Mzimba Rodney Simwaka, gulu la atolankhani la Hora Press Club, akulu akulu a kampani ya Raiply ndi anthu ena wokhuzidwa.
Ndipo Pafufupipi mitengo yokwana 1000 ndiyomwe inabzalidwa pa tsikuli.