Wanderers yalemba mphunzitsi wakale wa Bullets

Advertisement

Atatsanzika Mark Harrison, timu ya mpira wa miyendo ya Mighty Mukuru Wanderers tsopano yalemba mphunzitsi watsopano ophunzitsa osewera mu timuyi yemwenso anaphunzitsapo timu ya Nyasa Big Bullets Nsanzurwimo Ramadhan yemwe kwawo ndi ku Burundi.

Malingana ndi Chikalata chomwe chatuluka lero pa 14 febuluwale chotsimikizidwa ndi amene anali wa pampando wa olemba ntchito anthuwa a Tiya Somba Banda chaonetsanso kuti yemwe anali mphunzitsi wa timu ya dziko lino a Meke Mwase awalemba ngati othandizira mphunzitsi watsopanoyu.

A Ramadhan anaphunzitsaponso timu ya Wanderers mchaka cha 2001, Nyasa Big Bullets, Township Rollers, Amazulu, kiyovu, Black Leopards komanso anagwirizilapo timu ya Malawi ya Flames ndipo apa abwereranso.

Mnkhalakale ku Wanderers a Yassin Osman akhala wamkulu oyendetsa technical ndipo a Steve Madeira omwe anagwiraponso ndi timuyi m’buyomu awalembanso kukhala oyendetsa Timu pamebe otchinga pagolo wakale Simplex Nthara amulemba kukhala ophunzitsa ma goloboyi ndipo a Levi Mwale ndiwo akhale a zachipatala a Nyerere za ku Lali Lubani.

Chikalatachi chatsindikanso kulembedwa ntchito kwa a Bob Mpinganjira kukhala mpunzitsi wa Wanderers Reserve a Safarao Pompi , Lawrence Majawa ndi a Samuel Matukuta pa ma udindo ena.

A George Sangala awalemba kukhala mphunzitsi wa timu ya chisodzera ya wanderers mothandizana ndi a Darlington Misereni komanso a Samuel Matukuta omwe adzigwira ngati wazachipatsala ku wanderers Reserve komanso ku ya achisodzera.

Malingana ndi chikalatachi Ntchito za olembedwawa zayamba lero lomwe pa 14 February 2024, izi zikuchitika pamene ma timu ayamba kukonzekera mpikisano wa mu 2024.

Timu ya Wanderers yasintha zambiri mu timu yawo kutsatira kutuluka opanda chikho chilichonse mu mipikisano yonse ya mchaka cha 2023 zomwe mtsogoleri wa timuyi a Thom Mpinganjira anati mzokhumudwitsa.

Advertisement