Ana a m’ma 2000 akupwetekani – Wikise walangiza zimdya makanda

Advertisement
Malawi Music entertainment

Wa misala anaona nkhondo: Oyimba Che Wikise amene amadziwika kwambiri ndi nyimbo zowoneka ngati zoduka mutu koma za uthenga wa mphamvu, walangiza abambo onse a mvula za kale omwe samaugwira mtima akawona dilesi la ma buthu obadwa zaka za m’ma 2000 mpaka alowemo, kuti asamale apwetekedwa komaso ayalutsidwa.

Loweluka pa 3 February, 2024, Wikise yemwe anabadwa Frank Chawinga, watulutsa nyimbo yomvera komaso yowonera yomwe akuyitchula kuti ‘Amolo’ yomwe ili ndi malangizo akuya zedi, ndipo abambo osusuka onse akuyenera kudzimvera muntolo chifukwa nyimbo iyiyi muli mamasulidwe awo.

Munyimboyi, Wikise yemwe anayamba kutchuka ndi nyimbo ngati ‘Shabalakatari’ mchaka cha 2017 komaso anawonjezera moto ndi nyimbo ya ‘Chikam’phulikire’ mu 2019, wagwiritsa ntchito mdala yemwe wamutcha dzina loti ‘Molotoni’, mwachidule ‘Amolo’, yemwe akuchita zibwezi ndi asungwana anthete koma olimba mtima.

“Amolotoni, mukanapola moto/Amolo mukanapola fire/Ama 2000 akupwetekani a Molotoni/Ama 2 pin akuvulazani a Molotoni.

“Muli ndi banja a Molotoni, ndalama mukudya ndi slay-zo, kadyeni ndi ana ku nyumba, kadyeni ndi mama ku nyumba/Ana daily kudyera mtapasha, zikakhala zovala mzigamba, akazi anu chitenje nkwanyala, koma ku mowa ndinu a bayala/Siizi anava nkhwangwa ili m’mutu, ndi mnasi amakutsina khutu,” watelo Wikise mu kolasi komaso ndime yoyamba ya nyimbo ya ‘Amolo’.

Mukanema ya nyimboyi, zikusonyeza kuti mdala wankulu mimbayu, wathawa ku nyumba kwake atangolandira ngongole ya NEEF, kusiyana nkazi ndi ana ake chimanjamanja, akugona kumimba kukuliza malikhweru ndipo atapenga ndi chilembwe, anayamba kupezeka m’malo azisangalalo kumamwa mowa kwinaku akuchita kusaweruzika ndi asungwana omwe akuti ndiobadwa zaka za m’ma 2000.

Ku mapeto kwa zonse, ‘Amolo’ analipatsa buthu lochanuka m’masoli ndalama yokwana K20 miliyoni ngati chitseka pakamwa pomwe msungwanayu anawaopseza kuti aponya m’masamba anchezo zithunzi zolawura za awiriwa, ndipo posafuna kuyaluka bambo wakumwa madzi ometera ndevuyu anapelekadi ndalamayi.

Titamufusa za uthenga omwe akufuna kugwa kudzera mu nyimboyi, Wikise yemwe kangapo konse wawinapo mphoto kamba ka mayimbidwe ake opatsa chidwi, wauza Malawi24 kuti nyimboyi ndi langizo kwa abambo onse mdziko muno omwe akumapanga zibwezi ndi atsikana ang’onoang’ono.

“Nyimbo ya Amolo ndi langizo chabe kwa abambo omwe akukomedwa ndi atsikana omwe abadwa posachedwapa kuti asiye khalidweli. Choyambilira akuyenera kusintha kaganizidwe kawo ndipo akuyenera kuzindikira kuti uku ndi kupha komwe. Izi zikuchitikadi, choncho mu nyimboyi ndikupempha kuti chonde azibambo tiyeni tiyigwire mitima yathu,” watelo Wikise.

Wikise walonjeza onse omukonda kuti chaka chinoso apitilira kuwamwetsa wa mkaka ndi nyimbo zothyakuka bwino, zophunzitsa, zosangalatsa komaso zopeleka chilimbikitso ndipo wati posachedwapa akhala akutulutsa chimbale chake chomwe akuchitcha ‘Amolo’.

Pakadali pano anthu asonyeza kugwa mu chikondi kwambiri ndi nyimboyi kamba koti mumaola 20 oyambilira, nyimbo ya ‘Amolo’ yawoneledwa maulendo opitilira 56 sauzande pa YouTube, zomwe sizimachitika ngati nyimbo yayimbidwa mwa bwatabwata phuu!

Advertisement