Ndidalakwa chiyani, kepana ndisiye kuyimba? – wadandaula Temwa


Temwa Malawi Music

Patangodutsa maola ochepa woyimba wamkazi Tuno atadandaula za kusakondedwa, naye Temwa Gondwe wadandaula zomwezo ndipo akudzifusa kuti ‘Ndili kuti’ pomwe anthu ena awugogodi ayamba kumutoza

Chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke nyanga nchakuti, mkati mwasabatayi, Temwah yemwe ndimwini wake wa nyimbo ya ‘Mvetsera’ yomwe anaimba limodzi ndi Zeze ndipo chaka chatha yawonongetsa anthu ndalama, anayika pa tsamba lake la fesibuku chithuzi cha mwana wake wa miyezi isanu ndi umodzi.

Apa Temwa yemwe chaka chatha wakokolora mphoto za mnanu kamba ka mayimbidwe ake apamwamba, sanadziwe kuti wadzikodolera anthu onunkha nkamwa omwe monga zimachitira ntchentche zikaona chimbudzi, anakhamukira pa tsambali ndikuyamba kulavula zakukhosi, zomunyoza woyimbayu pamodzi ndi khanda lake losalakwalo.

Ndemanga zina zomwe tsamba lino lawona, anthu ena anayamba kufanizira mwana wa Temwa ndi katswiri oyimba chamba cha amapiano, Zeze Kingstone ngakhale kuti awiriwa pano samamwelana madzi pazifukwa zodziwa okha.

Mnyozo ngati uwu komaso zina, ndi zomwe zatutumutsa Temwa yemwe Lachinayi analemba pa tsamba lake la fesibuku kudandaula za kusakondedwa kwake ndi anthu ochuluka mdziko muno ndipo wafika pofusa kuti kapena zoyimbazi ayambe watenga kaye tchuthi?

“Koma mukuti ndinalakwa chani kweni kweni ? Mwina lelo mundiuze ndinvesese? Sindilimbana ndi munthu ndikabwela pa Facebook pano ndimapanga za nyimbo zanga generale I mind my own business but I don’t know how my life is offending some of you kuti mpaka mu muike mwana wanga zosamukhudza mwana achepelenji, so innocent as her mother ndapanga post just to appreciate my daughter Koma ayi ndithu ena akuipidwa nazo zimenezizi Koma Nde muneneni mwana kumpanga photo collage what for? Mwina tu tingosiya kuimbaku coz noo this is not on,” wadandaula Temwa.

Woyimbayu wati akudziwa kuti anthu ambiri akumupangira kaduka chifukwa choti zinthu zikumuyendera ndipo wati akudziwaso kuti anthu ambiri akupanga izi kamba koti akufunitsitsa banja lake lithe, zomwe wati sizinthu zabwino.

“Bwanji mumakwiya anzanu zikamawayendela ndi ufiti umenewo. Basi kukhosi mbeee Temwa asowe mtendele Temwa banja lake lithe Temwa ndi hule temwa this temwa that eh nakulakwilani chani????” Anateloso Temwa popitilira ndi uthenga wake pa fesibuku.

Pakadali pano masamba ambiri pa fesibuku akudzudzula chipongwe chomwe anthu akupangira oyimbayu ponena kuti izi zithakuwononga luso lomwe Temwa ali nalo kamba koti zili ndikuthekera koti atha kuyimba kudziyang’anira pansi komaso kubwelera mbuyomu pa mayimbidwe.

Chaka chatha, mtsutso unabuka pa masamba a nchezo pa nkhani yoti pakati pa Temwa ndi Zeze amene anatchukitsa mzake ndindani zomwe zinapangitsa oyimba awiri wa kusiya kuyimbira limodzi ndipo kenaka chidani cha khoswe ndi mphaka chidayambika komaso anthu ankatsutsana kuti kodi awiriwa chinali chibwezi kapena ankangoyimbira limodzi chabe?

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.