Sitinawachotse a Mutharika, latero bungwe la Mulhako


DPP president Peter Mutharika

Wapampando wa bhodi ya Mulhako wa Alhomwe watsutsa mphekesera yoti bhodiyi yachotsa mtsogoleri wakale wa dziko lino a Peter Mutharika ngati woyang’anira bungweli.

Mukuyankhula kwawo pa msonkhano wa atolankhani mu mzinda wa Blantyre lachiwiri,  Muchanakwaye Mpuluka yemwe ndi wapampando wa bhodiyi anati dongosolo ndi mphamvu zochotsa komaso kubwezeretsa amdindo mu bungweli zili ndi bhodi yaikulu imene imasankha komitiyi yosankha kapena kuchotsa amdindo.

Mpuluka wati ndi zabodza zimene nyumba zina zoulutsa mau zikulengeza kuti bungweli lachotsa a Munthalika pa udindowu.

“Bungwe lathu limalemekeza maganizo a aliyese. Mphamvu zopanga chiganizo sizikhala kwa munthu m’modzi ndipo izi zikapitirira tikasuma Ku bwalo la milandu,” atero a Mpuluka.

Iwo apatiriza kutsutsa mphekesera zonena kuti gulu lawo lagulitsidwa ku chipachi chomwe sanachitchure dzina.

Pa chochitikachi, ena mwa amene anali nawo ndi mkulu wa Mulhako wa Alhomwe Pius Mvenya, Felix Namagoya yemwe ndi wapampando mu chigawo cha kumwera komaso Felix Tambulasi yemwe ndi loya.

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.