Mwatilakwira — DPP yadandaula powotcheledwa nsalu

Advertisement
DPP members Malawi

Chipani cha Democratic Progressive (DPP) chati ndichodandaula ndi zomwe achita anthu ena omwe ang’amba komaso kuwotcha nsalu za chipani chawo ati kamba konyasidwa ndikuchotsedwa kwa a Kondwani Nankhumwa nchipanichi.

Lamulungu lapitali, anthu ena omwe ena mwa iwo anavala zovala za makaka a DPP, anatchingira nsewu a Nankhumwa pomwe amachokera ku mwambo wa mapemphero ku Ndirande munzinda wa Blantyre ndipo anthuwa anamukakamiza nkuluyu kuti awayankhule.

Malingana ndi kanema wina yemwe anthu akugawana m’masamba anchezo, ena mwa anthuwa anayamba kung’amba nsalu za chipani cha DPP ndipo kenaka anaziwotcha, ponena kuti iwo simamembalaso achipanichi kamba koti ndionyasidwa ndikuchotsedwa kwa a Nankhumwa nchipanicho.

Potsatira izi, chipani cha DPP chatulutsa kalata yomwe wasainira ndi oyankhulira wake a Shadric Namalomba omwe ati chipani ndichokhumudwa kwambiri ndi zomwe anthu otsatira Nankhumwa apanga pong’amba ndikuwotcha nsalu za chipani chawo.

“Chipani cha Democratic Progressive (DPP), chikudzudzula mwamphamvu kutenthedwa kwa nsalu zake ndi gulu la anthu omwe ndiotsata a Kondwani Nankhumwa. Ndale zolimbana ndi uchigawenga zomwe anthu otsatira a Nankhumwa awonetsa kudzera mumchitidwewu, ndi zakale kwambiri ku demokalase yamasiku ano.

“Mchitidwewu udawonetsa mkwiyo wawo kwa DPP potengera kuthamangitsidwa kwa a Nankhumwa mu chipanichi, DPP ikukhulupilira kuti chigamulo cha komiti yake yosungutsa mwambo, chinali choyenera ndi chovomelezeka,” yatelo mbali ina ya kalata ya DPP.

Chipanichi chatinso mchitidwewu ukuwonetseratu kuti otsatira a Nankhumwa samafuna Chitukuko, Chilungamo ndi Chitetezo zomwe ndi nsanamira za chipani cha DPP ndipo yatiso apa zikuonekeratu kuti anthuwa asiya kukhudzidwa ndi mavuto a nkhani nkhani omwe dziko la Malawi, kuphatikizapo iwo eni likudutsa.

DPP yalangiza mamembala ake kuti apewe kubwezera pa zomwe anthu otsatira Nankhumwa-wa achita ponena kuti chipani chawo chilibe nthawi yolimbana ndi ena koma chati chikuyang’ana njira zomwe zikufuna kuchiza dziko ku matenda akusayenda bwino kwa chuma.

Advertisement