Madera ena ku Nkhata-Bay mawayilesi samveka

Advertisement
Inside Malawi Radio station MBC radio 2

Anthu okwana pafupifupi 7,200 okhala m’madera ena akumidzi  m’boma la Nkhata-Bay alibe mwayi opeza mauthenga osiyanasiyana kudzera pa wailesi popeza mawayilesi samveka kumaderawa kuyambira nthawi ya atsamunda.

Madera monga Thotho, Mangw’ina, Musinjiyiwi, Chisangawe, Masasa, Chitundu komanso Sanji a Madera la mfumu yaikulu Khodza adakali mu mdima pa nkhani yokhudza ma mayilesi  komanso makina a intaneti.

Bambo Yotamu Mhone omwe ndi a zaka 60 okhala ku Dera la Thotho Mangw’ina akuti sanamverepo wayilesi ya mdziko muno ndipo wayilesi ya boma ya Tanzania (TBC) ndi yokhayo imene amamvera kumeneko.

“Tikupempha boma kuti litiikireko netiweki ya wayilesi komanso lamya kuti nafe tizitha kumvera mawayilesi kwathu kuno pomwe pano tikulephera kupeza mauthenga oyenera tikungokhala ngati obwera kuti timvera wayilesi yakunja,” anatero Bambo Mhone.

Ndipo mu mau ake Sub T/A Khoza inati: “Ine  ndipemphe  ku boma kuti ife kuno ku Thotho ndi madera ena ozungulira tipatsidwe mwayi womvera wailesi zakwathu komanso ma network, dera langa lino  kuyambira nthawi ya atsamunda mpaka pano takhala tikumvera wayilesi ya boma ya ku dziko la Tanzania -TBC Anthu ngati sakupeza mwayi wopeza nkhani ndizija anthu akumamva zamumaluwa,” anatero mfumu Khoza.

Nduna yazofalitsa nkhani komanso dijito omwenso ndi m’neneli wa Boma a Moses Kunkuyu anati: “Monga boma tivomeleze kuti ndi zoona anthu amaderawo sakumveradi mawayilesi wonse am’dziko muno ndipo bungwe la MACRA likudziwa kuti anthu ena m’madera ena a Nkhata-Bay amamvetsera wailesi za ku Tanzania. Izi zili choncho chifukwa cha m’mene malowo alili,” adatero a Kunkuyu.

Koma a Kunkuyu anaonjezera kunena kuti bungwe la MACRA linapereka chilolezo ku wayilesi zina za ku mpoto monga Voice of Livingstonia, Tuntufye Radio, Tigabane Radio, Wazilinda Radio zomwe zimatha kumveka madera ena ku Nkhata-Bay ko, komanso anati boma ndi lokonzeka kupereka ziphatso kwa anthu amene akufuna kuyambitsa ntchito za wayilesi ku Nkhata-Bay.

Zaka za m’mbuyomu, maderawa anavutika kwambiri ndi nthenda ya kolera, zomwe anthu ena akuti pakanakhala kuti anthu aderawa ali ndi mwayi womvera mawayilesi, mwina bwenzi amva zakapewedwe kamatenda wosiyanasiyana.

Ndizomvetsa chisoni kuti pomwe zinthu zamakono zilipo zambiri, anthu ena mdziko muno alibe mwayi  wopeza nkhani kudzera pa wayilesi.

Malo ngati awa ndiwo ali wofunikaso kwambiri kuyikako ma ICT center, Bungwe la MACRA likuyenera kuchita machawi ndi ndondomeko zoyika lamya ya mayilesi ku maderawa.

Advertisement