Ka chakudya tili nakoko tigawane, atero a Chakwera


Malawi President Lazarus Chakwera

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera apempha a Malawi kuti akondane pogawana ka chakudya kochepa kamene anthu ali nako mu nyengo ya njala ino yomwe imakhala miyezi yovuta kawirikawiri.

Poyankhula lero Ku Dowa pa bwalo la Andrew Murray ku Mvera atayendera Nyumba zomwe zikumangidwa za asilikali a nkhondo ku Mvera Support Batallion mu ulendo opita ku Salima, a Chakwera ati mkofunika kugwirana dzanja kuti tidutse m’nyengo ya mdimayi pogawana kamene kangapezekeko.

“Lero ndi nthawi yokuti aliyense agwire dzanja la mzake mkumanena kuti tiyeni tiolokere limodzi, lero ndi nthawi yakuti aliyense awonetsetse kuti tigwire ntchito molimbika kuti mawa likhale losiyana ndi m’mene dzulo linalili komanso m’mene lero lilili pakuti dzikoli tilibenso lina kwina lathu ndi lomweli” atero a Chakwera.

Mtsogoleriyu wati mpofunika kuchita zofunikira kuti dzikoli likhale losinthika monga m’mene likusinthikira pakali pano.

M’mawu ake, Mfumu yayikulu Chiwere ya M’bomali ati ku Dowa Njala yafika povuta kwambiri ndipo apempha kuti chimanga chidzifika mowirikiza ku delali kuti anthu apulumuke.

Mfumu Chiwere yatinso boma liganizile msanga ndondomeko yotapa Madzi ku Nyanja ya Malawi kupita ku Lilongwe ya Salima Lilongwe water project kuti ichite machawi kuti anthu a ku m’mawa kwa Dowa apindulenso pakuti mdelali madzi ndi ovuta kuwapeza.

Phungu wa delali a Richard Chimwendo Banda mmau ake anati dela lake ndi lokwera kotero mijigo sitheka ndipo anagwirizana ndi a Chiwere kuti ndondomeko yotapa Madzi ku Salima ikhala yofunika kwambiri kwa anthu a delali.

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.