Bushiri walengeza zogula ndege


Shepherd Bushiri

Mneneri Shepherd Bushiri yemwe ndi mtsogoleri wa mpingo wa ECG – Jesus Nation Church walengeza kuti akufuna kugula ndege yonyamula anthu obwera ku mapemphero ake kuchokera m’mayiko ena.

Izi ndi malingana ndi zomwe mneneriyu walemba pa tsamba lake la fesibuku lero Lachitatu pomwe wati lingaliroli labwera kamba koti akuona kuti ma kampani a ndege akumudyera masuku pa mutu.

Bushiri wati ndege yomwe akulingalira kugulayo ndiyoti izinyamura anthu omwe amabwera mdziko muno kuchokera mayiko akunja kudzakhala nawo pa mapemphero osiyanasiyana omwe iye amapangitsa makamaka munzinda wa Lilongwe.

“Ndili ndi malingaliro ofuna kugula ndege yoti idzinyamula anthu kubwera nawo ku mapemphero athu. Tikulemeletsa kampani za ndege,” watelo Bushiri muul uthenga omwe waulemba muchingerezi pa tsamba lake la fesibuku.

Anthu ambiri omwe akhamukira ku tsambali kukaikira ndemanga, ayamikira mneneriyu kamba kamaganizowa ponena kuti izi zithaso kuthandiza kupititsa patsogolo ntchito zokopa ulendo mdziko muno, pamapeto pake nkumapititsaso chuma cha dziko lino pa tsogolo.

Chithawireni mdziko la South Africa mchaka cha 2020, komwe a kuti kunali chiopsezo choti anakatha kuphedwa, Bushiri wakhala m’modzi mwa anthu komaso zinthu zomwe zapangitsa kuti dziko lino lizilandira alendo ochuluka ochokera m’mayiko ena.

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.