Botomani wati akudikira chibaluwa chosonyeza kuti amuchotsa m’chipani


M’modzi mwa anthu omwe athamangitsidwa mchipani chotsutsa boma cha DPP, Mark Botomani, wati zoti iye amuchotsa mchipanichi akungowerenga m’masamba amchezo ndipo iye wati akudikira kalata yochokera ku chipanichi yosonyeza kuti amuchotsa asanapange chiganizo chake pa nkhaniyi.

A Botoman ati ngakhale iwo ali ndi chikhulupiliro kuti chikalata chomwe chatuluka chochotsa anthu mchipanichi ndi chenicheni, iwo atemetsa nkhwangwa pa mwala kuti adikira kalata yawo kuchokera kuchipani yosonyeza kuti awachotsa.

A Mark Botomani omwenso ndi phungu wadera la Zomba, anafotokozanso kuti zoti awachotsa mchipanichi akungowerenga m’masamba amchezo.

A Botomani amayankhula izi kutsatira pomwe chipanichi chatulutsa kalata yochotsa anthu mchipani, ndipo wa mmodzi mwa iwo ndi a Botoman.