Apolisi asamutsidwa anamalira atatchingira nsewu mdipiti wa Chakwera


Patangodutsa maola ochepa pomwe anamalira anatchingira nsewu mdipiti wa galimoto za mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera mu nzinda wa Blantyre ndikuyamba kuyimba nyimbo zonyoza mtsogoleriyu, apolisi angapo amchigawo chakum’mwera asamutsidwa pa zifukwa zomwe ena akuti ndi kamba ka chipongwe chomwe tate wafukoyu wachitilidwachi.

Lachisanu lapitali, kunali chifwilimbwiti pa mphambano ya HHI munzinda wa Blantyre pomwe anamalira ena omwe ananyamula thupi la munthu wina lomwe amakaliyika m’manda a HHI munzindawu, anayimitsa mwachipongwe mdipiti wa galimoto zopelekeza mtsogoleri wa dziko lino, a Chakwera.

Pa nthawiyi, a Chakwera anali akuchokera ku nyumba ya chifumu ya Sanjika ndipo amathamangira ku bwalo la ndege la Chileka komwe amafuna kukakwera ndege paulendo wawo opita mdziko la Democratic Republic of Congo komwe akuti ayitanidwa mwadzidzi ndi mtsogoleri wa dzikolo.

Anamalirawa anayimitsa mdipitiwu ndikuyamba kuimba nyimbo za chipongwe, amvekele: “Mbuye timenyereni nkhondo kulimbana ndi satana, ali ndi zida zowopsa,” kenaka nkudzayamba kuimba kuti; “waimabe waimabe waimabe” kwinaku atawunjikana pakati pa nsewu wa Magalasi, kuchititsa kakasi nzika yoyambayi yomwe siikanachitira mwina koma kudikira kaye kwa mphindi zingapo.

Koma patangodutsa maola ochepa a Chakwera atachitidwa chipongwechi ndi anamalira okwiyawa, anthu kucha kwa loweluka pa 20 January, 2024, anadzidzimutsidwa ndi chikalata chomwe nthambi ya apolisi yatulutsa chomwe chikusonyeza kusamutsidwa kwa akuluakulu angapo apolisi nchigawo chakum’mera.

Mwachitsanzo, a Richard Luhanga mwe anali mkulu wa apolisi (Commissioner) mchigawo chakum’mwera kumadzulo, wasamutsidwa ndipo akupita mchigawo chaku mpoto pa udindo omwe anali omwewo ndipo m’malomwawo mwaikidwa a Noel Kaira omwe anali ku mpoto komwe akupita nzawoko.

Mbali inayi, mkazi wa a Luhanga, Rhoda Luhanga, yemwe anali Regional Operations Officer 2 mchigawo chakum’mwera, akhala akupitaso ku mpoto kukagwira ntchito ngati Regional Operations Officer 3.

Ngakhale kuti chikalatachi chomwe wasainira ndi mkulu wa nthambi ya apolisi a Merlyne Yolamu, chikusonyeza nsamutso wa apolisi enaso mchigawo cha pakati, anthu achita chidwi kwambiri ndikusamutsidwa kwa akuluakulu anchigawo chakum’mwerawa.

Anthu ena makamaka m’masamba a nchezo, ati akuganiza kuti izi zachitika kamba ka chipongwe chomwe mtsogoleri wa dziko linoyu wachitilidwa ndi anamalirawa ponena kuti apolisiwa analephera kuonetsetsa kuti mtsogoleri wa dzikoyu sanachititsidwe manyazi mwa mtunduwu.