Phungu wa Zomba Malosa wagona ku ma ofesi a Works Training Center kufuna chimanga

Advertisement
Grace Kwelepeta Zomba

Phungu wa mdera la Zomba Malosa Grace Kwelepeta wagona kuma ofesi a Zomba Training Center kufuna kukakamiza galimoto yayikulu  yomwe yanyamula chimanga chogawira anthu mwaulele omwe akuvutika ndi njala kuti ipite mdera lake.

Kwelepeta wauza Malawi24 kuti chiyambireni Boma kugawira anthu chimanga mu mwezi wa October chaka chatha anthu a mdera lake alandira kamodzi kokha ndipo wati ndidzokhumudwitsa popeza madera ena aphungu alandira kambiri mbiri.

Iye wati mdera lake la Zomba Malosa anthu akugona ndi njala chifukwa chosowa chakudya ndipo wati ali ndi nkhawa popedza ntchito yogawa chimanga chawulere yomwe Boma lidakhadzikitsa itha mwezi wamawa wa February zomwe zikusonyedza kuti anthu amdera lake apitilirabe kuvutika ndi njala komanso sapindura ndi ntchitoyi.

Atafunsidwa ngati Bwanamkubwa wa boma la Zomba akudziwa zankhaniyi, Kwelepeta adati wakhala akupita ku Office ya Bwanamkubwayu kukapereka madandaulo amomwe chimanga chikagawidwira koma sizikuthandidza kanthu.

“Mdera langa anthu amagonera mango chifukwa chosowa chimanga koma tsopano poti mango atha ayamba kugona osadya moti ana ambiri sakupita kusukulu chifukwa chosowa chokudya ndiye ndipemphe Boma kuti atithandidze ndi chimanga,” adayankhula motero Grace Kwelepeta.

Pamenepa Phunguyu wapempha mabungwe, makampani komanso anthu akufuna kwabwino kuti athandidze anthu amdera la Zomba Malosa ndi chokudya popedza mdera lake lidakhudzidwa ndi Namondwe wa Freddy.

Boma lidakhazikitsa ntchito yogawa chimanga chaulere kwa anthu omwe alibe chokudya mwezi wa October chaka chatha ndipo ntchitoyi ikuyembekedzereka kutha mwezi wa February chaka chino

Advertisement