Nyumba ya boma yachotsa wothilira maluwa pomuganizira kuti amaulura zinsinsi


State House in Lilongwe is the official residence of President of Malawi.

Mayi yemwe amagwira ntchito yosamala maluwa a Tiyanjane Mlangeni, omwe akuganizilidwa kuti ndiosasunga pakamwa ndipo akhala akuwulura zinsinsi zochuluka zokhudza kumpanda, inde ku nyumba ya boma, achotsedwa ntchito.

Izi ndi malingana ndi kalata yomwe boma latulutsa yomwe wasainira ndi Shadreck L Ching’oma m’malo mwa mlembi wankulu wa boma a Colleen Zamba yomwe ikusonyeza kuti a Mlangeni achotsedwa ntchito lachitatu pa 27 December, 2023.

Chikalatachi chikusonyeza kuti a Mlangeni omwe adalembedwa ntchito ngati wosamalira pa bwalo komaso maluwa (gardener) ku nyumba ya boma, chaka chatha anachenjezedwa kamba kowulura nkhani zokhudza ku nyumbayi.

Mayiyu akuti chaka chatha mu December analankhura monyoza nkhani yokhudza mphatso za chikondwelero cha khilisimisi zomwe akuluakulu a ku nyumba ya bomayi anapeleka kwa ogwira ntchito awo ndipo ataitanidwa kuti akalangizidwe anavomeleza kulakwitsa ndipo anachenjezedwa kuti asadzayambileso.

Koma poti wachake ndi wachake, chaka chino Mlangeni akuti wakhalaso akuwulura nkhani zosiyanasiyana kudzera pa masamba a nchezo ndipo a kuti mayiyu wabweretsa chisokonezo ku nyumba yolemekezekayi, zomwe zapangitsa akuluakulu kuti angoganize zomudomola.

“Zolemba zathu zikuwonetsa kuti pa 13 Julayi, 2023 mudapatsidwa kalata yochenjezedwa, Ref. No SR/RDM CONF/01A potsatira kuvomeleza kwanu mutaitanidwa kuti mukayankhe pa nkhani yokhudza momwe mphatso za khilisimisi zinapakilidwira.

“Ndizodabwitsa kuti lipoti laposachedwa lomwe ofesiyi yalandira kuchokera kwa a Chief of Staff likusonyeza kuti mwezi uno wa December, 2023, mwalemba komanso kufalitsa pa masamba a nchezo mawu angapo odzudzula akuluakulu ogwira ntchito ku State Residences ndipo izi zabweretsa chisokonezo ku State Residences.

“Ndikulemberani kukudziwitsani kuti motsatira Ndime III ndi IX ya pangano lantchito lomwe mudasaina ndi Boma komanso mogwirizana ndi gawo 59 (1) (a) la Employment Act, ntchito zanu monga Horticulture Assistant (Grade M), sizikufunikiraso ndipo zathetsedwa kuyambira pa 27 Disembala, 2023,” yatelo mbali ina ya kalatayi.

Kalatayi yati mayiyu apatsidwa malipiro a mwezi umodzi m’malo mwa chidziwitso, molingana ndi Ndime IX ya mgwirizano wantchito komaso atu alandira chiwongola dzanja cha 15%.

Pakadali pano a Mlangeni aw u za nyumba zona zofalitsa mawu kuti iwo sakugwirizana ndi zifukwa zomwe awachotsera pantchito chifukwa ulendo uno sadawaitane kuti akamve mbali yawo.

Mu ma odiyo omwe atuluka pa masamba a nchezo sabata ino, Mlangeni amauza mabwana awo kuti ku nyumba ya boma kuli anthu ena akumakatenga ndalama ku bungwe lotolera misonkho la MRA pogwiritsa ntchito dzina la State House.

A Mlangeni anatinso anthu ena ogwira ntchito ku State House amakhalira kuba zakudya monga nyemba ndi nyama.