Madera ena kukhala madzi osefukira sabata ino – yatelo MET

Advertisement
Mvula Malawi

Unduna owona za chilengedwe ndi kusintha kwa nyengo, mogwirizana ndi nthambi yowana za zanyengo, wati pali chiopsyezo choti sabata ino madera ena m’dziko muno makamaka mchigawo cha kum’mwera kukhala madzi osefukira.

Izi ndi malingana ndi kalata yomwe undunawu komaso bungwe la MET latulutsa Lachitatu pa 27 December, 2023 yomwe ikufotokoza za chiopsyezochi chomwe akuti ndi kamba la mvula ya mphamvu yomwe yayamba kale kugwa m’madera ochuluka mdziko muno.

Chikalatachi chikusonyeza kuti ena mwa madera omwe angakhudzike kwambiri ndi madzi osefukirawa, ndi maboma a mchigawo chakumwera omwe ndikuphatikizapo Mwanza, Zomba, Mulanje, Phalombe, Blantyre, Chikwawa komaso boma la Nsanje.

Ndipo mbali inayi bungwe la MET lati ena mwa madera omwe angakhuzidwe mocheperako, ndi maboma amchigawo chakumpoto komaso ochepa chigawo cha pakati omwe ndi kuphatikizapo boma la Lilongwe, Karonga, Rumphi komaso Mzimba.

Pakadali pano undunawu komaso bungweli lalangiza anthu mdziko muno makamaka madera omwe ali pa chiopsyezowa kuti apewe zinthu zomwe zingapangitse kuti pakhale kuluza miyoyo monga kuoloka mitsinje yomwe ndiyosefukira.

“Chiopsyezo cha kusefukira kwa madzi ndi chachikulube pamene mvula yamphamvu ikupitilira choncho tikulangizidwa kuti tipewe kuoloka pamene madzi asefukira kapena akuthamanga kwambiri,” yatelo kalata yochoka ku MET komaso ku unduna wa zachilengedwe.

Anthu akulimbikitsidwaso kuti nthawi zonse adzivera komaso kutsata zomwe nthambi ya zanyengoyi imatulutsa ndicholinga choti ngozi za mtunduwu zidzitha kupewedwa.

Advertisement