Nyimbo ya malemu Atoht Manje ‘Nchape’ yaoneledwa ka 1.1 miliyoni pa YouTube

Advertisement
Munthu' hitmaker Atoht Manje real name Elias Missi has died.

Pofika lero pa 27 December 2023, nyimbo ya Atoht Manje yomwe mutu wake ndi ‘Nchape’ tsopano yaoneledwa ka 1.1 miliyoni pa YouTube mu miyezi iwiri yokha.

Iyi ndi nyimbo ya Atoht yomwe yaoneledwa kwambiri pa nyimbo zomwe oyimbayu anaika pa tsamba lake la pa Youtube. Nchape inalinso nyimbo yomaliza yomwe Atoht anatulutsa asanamwalire.

Katswiriyu  adamwalira m’mwezi wa October chaka chino pamene iye adapita ku University of Livingstonia m’boma la Rumphi komwe amkakayimba.

Patsikuli malemuwa adamva kutentha kwambili. Apa anawatsanzika kaye anzake kuti akupita kaye mugalimoto basitu katswiriyu omwewo udali ulendo wakumsabwera.

Malemu Atoht Manje adali munthu m’modzi amene amadziwa kucheza ndikukhala bwino  ndi anthu.

Kutengera luso lake, katswiriyu wayimbapo nyimbo zosiyanasiyana zomwe a Malawi ambili akhala akusangala nazo. Zina mwa izo ndi Tizipepese, Kunong’a, Huwa, Ndalama, komanso Zilibwino.

Mzimu wakatswiliyu upitilize kuwusa mumtendere.

Advertisement