Chaka chopanda dipo! Mzungu wayinyumwa


“Osewera tagwirizana kutenga zikho zonse,” mhuuu! Anakadziwa sanakayankhula, maloto a chumba enieni, chimanjamanja ikutuluka m’chakachi. Tsoka la mfutso lopita pa moto kawiri ndipo kupsa kwake ndi kwa chigumu, pansi ndi pa mwamba. Mukutipheranji? Walira movetsa chisoni neba. Khilisimisi yalephereka ku Lali Lubani.

Osewera a timu ya Mighty Mukuru Wanderers atagwirizana ku mayambiliro a chakachi kuti timuyi itenge zikho zonse chaka chino, titha kutsimikiza kuti zinali nkhamba kamwa chabe kamba koti m’manja muli yede, timuyi ya kwangula chakachi, ndipo ikudziguguda pa mtima mkumati chakachi chinkalinda kuteleku?

Powona m’mene timuyi inachitira ku mayambiliro a mpikisano wa FDH, ochemelera awo anali ndi chiyembekezo kuti zikho zinayi zija zikupitadi ku timu yovala za makaka “blue” yi, koma mumkuphethira kwa diso, zinayang’ana ku dazibomu, inatuluka mumpikisanowu itagonja ndi chigoli chimodzi cha nkwelekwete ndi timu ya Mafco pa bwalo la Kamuzu munzinda wa Blantyre.

Zitatelere timuyi inayika chidwi chaka ku ligi ya TNM ndipo momwe imadodera chikopa imapeleka chilimbikitso kuti chikho ichi chokha sichiwapitilira, koma mhuuu! Maloto anathera m’mazira. Timuyi inathera pa nambala yachitatu kamba koti Silver Strikers inalumira mano mpaka kuwajudula pa nambala yachiwiri yomwe anamerapo mizu.

Paja akulu anati ikakuwona litsilo siyikata, malodza a mpikisano wa Airtel ndi iwa akumvawa, Noma inatuluka mumpikisanawu mwa chibudu potsatira chipwilikiti chomwe chinachitika pomwe ankasewera ndi ‘Ma bankers’ pa bwalo la Bingu m’mwezi wa September zomwe zinapangitsa kuti timuyi ilumile mano zotenga chikho cha ndalama phwamwamwa, Castel.

Komatu zavuta ku mpanda! Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yawonetsa nsana wa njira neba, inde kumuyatsira nyali dzuwa lili phwee. Ndipo zatsimikizika kuti ndizosatheka atambala awiri kulilira khora limodzi, zafa mwachibudu Nyerere pa bwalo la Kamuzu zomweso zapangitsa kuti maloto otenga zikho zonse aja atitimile, yamaliza chakachi opanda dipo.

Chomwe chaswa mitima ya ochemelera timu wa Noma nchakuti, pomwe imasewera ndi Bullets Lamulungu, inali ndi mwayi onse ogonjetsa mphangala zinzawozi koma osewera awo kangapo konse analephera kugwilitsa ntchito mwayi wa nzama ofukula ndi manja omwe anaupeza. Anaphonya kwambiri osewerawa moti ochemelera timuyi anakhalira kumangoti hiiii! Aaaa! Kusavetsetsa ndi kuphonyako.

Pomwe osewera, akuluakulu komaso otsatira timuyi amapukuta misozi yomwe imatsikira m’masaya mwawo potsatira kufa kudzera pa mapenate ndi Maule, naye mphunzitsi wa timuyi, Mark Harrison, anathira tsabola pa mabalawo pomwe analengeza kuti watula pansi udindo wake ku timuyi.

Malingana ndi chikalata chomwe Harrison watulutsa timuyi itangoluza ndi Bullets, chomweso chikusonyeza kuti chinalembedwa pa 19 December, 2023, chiganizochi wachipanga kamba ka zifukwa zosiyanasiyana zomwe sanazitchule zomwe akuti zikuchitika mu timuyi komaso m’masewero a mpira wa miyendo mdziko muno.

Pakadali pano, manong’onong’o akumveka kuti timuyi ikuchita zokambirana ndi mphunzitsi wakale wa timu ya dziko lino Flames, a Meck Mwase komaso Alex Ngwira kuti ayambe kuphunzitsa osewera ndi cholinga choti chaka chikubwerachi akolore zokoma.